Ulamuliro wa Mulungu - Free Grace Evangelistic Association
Transcrição
Ulamuliro wa Mulungu - Free Grace Evangelistic Association
Ulamuliro wa Mulungu Pomwe pali Mawu a Mfumu, pamakhala Mphamvu. Wolemba I.A. Sadler Ulamuliro wa Mulungu Wolemba I.A. Sadler Copyright . I. A Sadler 2011. Lachingerezi linasindikizidwa ndi: Free Grace Evangelistic Association (Zambia) P.O. Box 81277, Kabwe, Zambia Email:[email protected] ww:freegrace-ea.org La Chichewa lasindikizidwa ndi: Assemblies of God Press,5749, Limbe Malawi. M’malo mwa Free Grace Evangelistic Association (Malawi) P.O. Box 502, Balaka, Malawi. Email: [email protected] Mavesi a Mawu a Mulungu omwe agwiritsidwa ntchito. Mavesi a Mawu a Mulungu omwe agwiritsidwa ntchito atengedwa mu ‘BUKU LOPATULIKA NDILO MAWU MULUNGU’ losindikizidwa mu chaka cha 1997. Ili ndi Baibulo lomwe wolemba anapeza kuti linamasulidwa monga la chingerezi la King James Version la m’chaka cha 1611, lomwe liri ndi dalitso loposa la Mulungu. Wolemba wina aliyense yemwe angafune kuti adziwe zambiri za izi angathe kuwerenga mabuku omwe anasindikizidwa ndi Trinitarian Bible Society (Tyndale House, Dorset Road, London, SW19 3NN, England), monga buku la ‘The Old is Better’ ndi (Gospel Standard trust), buku lomwe adalemba Dr E. Hills lotchedwa ‘The King th James Version Defended’ (4 Edition; ISBN 0-91592300-9). ZAMKATIMU. 1.Chidziwitso …………………………………………………………………………………. 1 Chiweruzo chiyenera kuyambira mu Nyumba ya Mulungu……. Kodi liwu lakuti “Ulamuliro” litanthawuza chiyani?. 2.Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi…………………………. 4 Pachiyambi Mulungu …… Kuwukira Kotsutsa Ulamuliro wa Mulungu …… Kutumikira Cholenegdwa kapena Mulengi ….. Amene akonda Mulungu zonse zithandizana kuwachitira ubwino. 3.Ulamuliro wa Mawu a Mulungu…………………………………... 11 Lamulo Loyera la Mulungu ….. Mphamvu ya Uthenga Wabwino ….. Lalikira Mawu ….. Gwiritsani Mawu Okhulupirira a Chowonadi. 4.Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo…………………. 19 Kuwukanso kwa Akufa ….. Chikhululukiro cha Machimo ….. Ulamuliro pa Mpingo ….. Utumiki wa Wukulu wa Kulalikira. 5.Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu…………………… … 28 Ndondomeko mu Mpingo wa Khristu ….. Ndondomeko mu banja ndi Dziko. 6.Chitsimikizo cha Ulamuliro Wotsiriza wa Mulungu…………… 33 Munthu Ayenera Kuyankhapo Mulandu ….. Kubwera kwa Chiwiri kwa Khristu ….. Kumaliza. Ulamuliro wa Mulungu. MUTU 1. CHIDZIWITSO. Chiweruzo chiyenera kuyambira mu nyumba ya Mulungu. Mu Chipangano Chakale pa nthawi yomwe Oweruza amatumikira, timawerenga kuti; “Masikuwa panalibe Mfumu m’Israeli, yense anachita chomuyenera m’maso mwake”(Oweruza 17:6). Zowonadi tikuziwona izi zikukwaniritsidwa masiku ano, osakhala mu nyumba za anthu ndi mu dziko, komanso ngakhale mu mipingo. Wina angathebe kufunsa kuti “Kodi mipingo ndi Akhristu sanalandire mu masiku ano a Chipangano Chatsopano vumbulutso la Yesu Khristu, yemwe ali Mfumu ya Mafumu ndi Ambuye Wa Ambuye?” Inde izi ndi zowona; koma kodi vumbulutso lodalitsikali lalandiridwa motani? M’mutu kapena mu mtima? Mu thupi, kapena mwa Mzimu Woyera? Kodi Mulungu akulemekezedwa mu milomo, kapena mokhulupirika kuchokera mu mtima? Zipatso za uchimo mu masiku athu, ndi kosasamalira kwa Ulamuliro wa Mulungu ngakhale mu mipingo ya Mulungu yomwe amavomereza ndi kuchita malamumbiro, zowona zotsimikizika ndi zakuti ambiri sadziwa Mulungu mu Mzimu ndi chowonadi, kapena ngati adziwa, abwerera m’mbuyo ndi kuti ali akugona. Wina angathe kufunsa; “Nanga ndi chifukwa chiyani pali kusasamala Ulamuliro wa Mulungu ndi kunyoza dzina lake loyera mu dziko komwe kulipo pa anthu osatembenuka mtima?” Inde, ndipo tifika ku nkhani iyi kutsogoloku. Nanga ndi chifukwa chiyani dzina la Ambuye linanyozedwa pakati pa ochimwa? Kodi sichinali chifukwa cha chinyengo cha iwo omwe amavomereza dzina la Ambuye, omwenso amadzikweza chifukwa cha chipembedzo chawo ndi kuti ndi obadwa ochokera ku fuko la Abrahamu? (Aroma 2:17-24). Mtumwi Petro analemba kuti; “Chiweruzo chiyambe pa nyumba ya Mulungu” (1 Petro 4:17); chomwechonso ndi momwe zikhalire mu buku ili. Kodi nanga Ulamuliro wa Mulungu si ukusamaliridwa motere bwanji ndi ambiri omwe ali Akhristu ovomereza Yesu? Tikuyankha motere kuti ndi 1. Ulamuliro wa Mulungu. chifukwa cha kusamvera Mawu a Mulungu. Chifukwa chiyani nanga? Chifukwa chikondi cha ambiri chazilala. (Mateyu 24;12). Pali chosowa chachikulu cha chikondi cha uzimu chomukonda Mulungu chomwe chitsikira kuchoka ku chikondi cha ulemerero cha Khristu kupita kwa ochimwa chomwe chiwonetsedwa mu moyo Wake, ndi mu imfa Yake ya pa mtanda ndi chomwe chinavumbulutsidwa kwa ife ndi Mzimu Woyera. Awa ndiye maziko ndi mphamvu ya kumvera Uthenga Wabwino, “Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.” (Yohane 14:15); ndi “Tikonda ife chifukwa anayamba Iye kutikonda.” (1 Yohane 4:19). Momvetsa chisoni, ambiri lero sali okhudzidwa ndi nkhani ya kumvera monga mwa ndondomeko za masiku ano, dongosolo la mipingo, ndi miyambo: mawonekedwe a uMulungu omwe amalola zambiri za zokondweretsa za dziko la pansi kuti angathe kumachita popanda kuletsedwa, kudzikundikira chuma chambiri pa dziko la pansi kuti apititse patsogolo moyo wa wofuwofu. Koma nanga chikumbu mtima chathu chimatikantha ife? Kodi tiribe makutu kuti timve chomwe Mzimu akulankhula ku mipingo? Kodi Ambuye Yesu Khristu sananene kuti; Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku nanditsate Ine” (Luka 9:23). Kodi sitimanthunthumira pa fanizo la wofesa, pomwe Ambuye anachenjeza za mbewu zomwe zinagwera pa minga?” Ndipo ena ndiwo akufesedwa kuminga, iwo ndiwo amene adamva mawu, ndipo malabadiro a dziko la pansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mawu, ndipo akhala opanda chipatso” (Marko 4:1819). Kodi tikuwumitsidwa mitima lero mu chipembedzo cha ufulu kotero kuti tikukhala mu moyo wa kuwukira kutsutsana ndi Mulungu, koma tikufunafuna kuwoneka a chipembedzo chosawonongeka cha chikhristu? Chosowekera chachikulu chomwe tiyenera kuchifufuza ndi chifundo cha Mulungu mu chikhulupiliro chowona ndi kulapa. Kodi liwu lakuti “Ulamuliro” litanthawuza chiyani? Tisanalowe kwathunthu mu phunziro ili, tiyenera kuti tipeze tanthawuzo la liwu lakuti “Ulamuliro”. Likutanthawuzidwa mu buku la Mtanthawuza Mawu kuti “Mphamvu kapena ufulu wakukakamiza kumvera”. ( Concise Oxford Dictionary, 8th Edition ). Pomwe liwu Lakuti “ulamuliro” likupezeka mu Baibulo, mawu omwe latanthawuzidwako amamasuliridwanso malo ambiri 2. Ulamuliro wa Mulungu. monga “mphamvu” komanso mu malo ena monga “nyonga”, “ulamuliro wa kukhazikitsa chilamulo”, “ufulu”. Tiyeni tsopano mwapang’ono tiyang’ane ndi kulingalira pa zitsanzo zochepa. Khristu anaphunzitsa “monga mwini mphamvu” (Marko 1:22), ndipo “ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imumvera Iye” (Marko 1:27). Komabe, mawu omwewo mu chiGriki omwenso mu chingerezi atanthawuza “ulamuliro” mu Marko 1, amatathawuzidwanso “mphamvu” ku Marko 2:10, pokamba mokhudzana ndi chikhululukiro cha machimo, “mwana wa munthu ali nayo mphamvu pa dziko la pansi yakukhululukira machimo”. Mawu a Mulungu awo ali chitsimikizo cha uMulungu wa Khristu, yemwe anali “Mulungu Iye amene anawonekera m’thupi”. (1 Timoteyo 3:16). Apa tikuwona kuti pamene tilingalira za ulamuliro wa Mulungu, tiyeneranso kulingalira za mphamvu yake, nyonga, ufulu ndi kukhazikitsa chilamulo kwake pa zinthu zonse za pa dziko ndi za kumwamba, za kuthupi ndi za uzimu, kaya ndi za kanthawi kapena za muyaya. Mulungu ali osiyana ndi ma udindo a ulamuliro wa umunthu, yemwe, ali bambo ndi mayi ochimwa chabe, ali ndi malire mu mphamvu ndi chilungamo (monga okhazikidwa ndi kuloledwa ndi Mulungu). Komabe, mphamvu ya Mulungu iribe malire, ndipo ulamuliro wa Mulungu ndi wathunthu; palibe chimene chimazemba chilamulo chake. Ngakhale mfumu yayikulu Nebukadinezara anafikitsidwa pa kuvomereza Mulungu; “Ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam’mwambamwamba, ndi kumuyamika ndi kumuchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamuilira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwo mibadwo; ndi okhala pa dziko la pansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake mkhamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko la pansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?” (Daniel 4:34-35). Ambuye Yesu Khristu wowuka kwa akufa analengeza kwa ophunzira: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine kumwamba ndi pa dziko la pansi” (Mateyu 28:18). Apa tikuwona kuti mphamvu ndi ulamuliro ndi zimodzi ndipo zimakhala za mngwiro mwa Khristu Yesu. Ngati ife titamvetsetsa za mphamvu ndi ulamuliro wa Mulungu m’modzi mwa Atatu, sitikadachitenga chipembedzo ndi kuvomereza kwa dzina la Ambuye Yesu Khristu kukhala zinthu za phindu lochepa ndi kusazipatsa ulemu woyenera. 3. Ulamuliro wa Mulungu. Anthu osawuka ochimwa oyenera kupita ku gahena, omwe aphunzitsidwa ndi Mzimu Woyera kuti alilire chifundo, amakokedwa ndi mphamvu ndi ulamuliro wa ulemerero wa chiyembekezo mu chipulumutso chomwe mphamvu zonse ndi ulamuliro wonse zigonera mwa Yesu, yemwe anawakonda iwo nawakhetsera mwazi wa mtengo wapatali. Ali ndi mphamvu ndi ulamuliro wa kukhululukira machimo awo. Amayenera kungolankhula mawu, ndipo iwo amapangidwa kukhala angwiro mwathunthu. Analonjeza; “Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu”. (Mateyu 7:7). MUTU 2 ULAMULIRO WA MULUNGU MONGA MLENGI. Pachiyambi Mulungu. Mitu yoyambirira ya Baibulo ili ndi maziko omwe Mawu Olembedwa onse amamangidwapo. Masiku ano anthu amanena kuti Mawu Olembedwa Oyambirira opezeka mu Genesis ali nkhani wamba kapana zizindikiro chabe osati kuti ndi chowonadi monga momwe zinalembedwera. Ngakhale kuti chowonadi cha kulenga kwa Mulungu ziri ulamuliro wake monga Mulengi “chawonekera mkati mwawo pakuti Mulungu anachiwonetsera kwa iwo”. (Aroma 1:19), komatu munthu wochimwa ali mu kuwukira kowonetsera. Kukana kwa kusalakwika ndi chowonadi cholembedwa cha buku lonse la Genesis limalimbana ndi mtima pa za chiphunzitso cha ulamuliro wa Mulungu, ndi chowonadi chokhazikika chomwe chikhazikitsa umwini mphamvu wa Mulungu. Mwa tsoka, okhulupirira ndi akhristu ambiri ovomereza Khristu agwedezeka ndi zomwe a sayansi amenena za kusintha kwa chilengedwe pakupita kwa nyengo. Ena anayesera kuphatikiza za kusinthikazi ndi Baibulo, kuyesayesa kuti alumikize zinthu zomwe sizingalumikizike nazo popeza ndi zosiyana. Ena agwira ntchito kwambiri pofufuza ndi kuyesa zonse zomwe a sayansi azipeza zomwe ziri zogwirizana ndi chilengedwe. Pomwe ziri zosakayikitsa pa kufunika kwa kudziwa za matsutsano zomwe a sayansi amanena pakukhulupirira za sayansi motsutsana ndi zopanda nzeru ndi zongoganiza za nkhani ya kusintha kwa zinthu pakupita kwa nyengo, 4. Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi. tisowa zoposa ngakhalenso zabwino kwambiri zomwe Akhristu angapereke; tisowa chikhulupiriro chopatsidwa ndi Mulungu. (Aefeso 2:8). Posakhala nacho ichi, sitidzakhulupirira moyenera ndi kumvetsa za Ulamuliro wa Mulungu monga Wolenga. “Ndi chkhulupiriro tidziwa kuti mayiko ndi a m’mwamba omwe anakonzedwa ndi Mawu a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwa zochokera mwa zowonekazo. Koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo ndipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.”(Ahebri 11:3,6). Chomwecho chikhulupiriro chidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mawu a Khristu.” (Aroma 10:17). Timadalira kwathunthu pa Mulungu kulankhula mawu a mphamvu mu mitima yathu. Pokhapokha alankhule, ife timakhala mu mdima. Likhale pemphero lathu ndi chokhumba chathu kuti Mulungu athe kulankhula monga adachita pa tsiku la kulenga. “Ndipo anati Mulungu, “Kuyere; ndipo kunayera.”(Genesis 1:3). Komatu tili nawo Mawu a Mulungu olembedwa akuti ophunzira a Yesu anadza kwa Yesu napempha kuti awawonjezere chikhulupiriro (Luka 17:5). Timawerenganso za m’modzi yemwe analira mu kuvutika kwake; “Ambuye ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.” (Marko 9:24). Ndipo Ambuye amamva kulira kwa a umphawi. Chifukwa chake, monga Yesu Khristu ali “yemweyo dzulo, ndi lero, ndi ku nthawi zonse.”(Ahebri 13:8), tiyeni potero ifenso tidze kwa Mulungu mogonjera ku chifuniro chake cha pamwamba. Mwa kulapa, kudandawulira mu dzina la Yesu kuti mphatso ya mtengo wapatali ya chikhulupiriro ipatsidwe kwa ife mwa Mzimu Woyera. Titafunafuna ndi mtima wogonja ndi kulapa, apo ndiye pamakhala umboni weniweni wakuti timalandira ulamuliro wa Mulungu. Komabe, ngati tingafike pamaso pa Ambuye modzikuza kapena mopanda ulemu, kapena kupemphera momulamula Ambuye monga ngati tiyenera kena kali konse, apa ndiye kuti tikukana ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi wathu wamphamvu yonse. Mawu a Mulungu amanena momveka bwino za iwo omwe Ambuye amawayang’ana mu chifundo. “Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko la pansi ndi choyikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti? Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinawoneka, ati Yehova; koma ndidzayang’anira munthu uyu amene ali wa unphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mawu anga.”(Yesaya 66:1-2). 5. Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi. Buku la Genesis limayamba ndi kufotokoza za momwe Mulungu analengera zinthu zonse, zomwe zinakhudza onse Atatu mwa Mulungu kuti analenga kumwamba ndi dziko la pansi. Dziko la pansi ndipo linali lopanda kanthu, ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unafungatira pamwamba pa madzi. (Genesis 1:1-2). Ndipo keneka timawerenga za momwe Mulungu analengera china chiri chonse, “ndipo anati Mulungu;” izi zilankhula za Mawu, Mwana wa Mulungu. Paulo akulankhula za Mwana; “Amene ali fanizo la Mulungu wosawonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse; pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za pa dziko, zowoneka ndi zosawonekazo, kapena mipando yachifumu, kapena ma ufumu, kapena ma ukulu, kapena ma ulamuliro, zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye. Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana mwa Iye.” (Akolose 1:15-17). Zowonadi, ulamuliro wa Mawu a Mulungu wakhazikitsidwa kuyambira pachiyambi pa Mawu Olembedwa, ndipo ali maziko a chowonadi kuyambira ku Genesis mpaka Chivumbulutso. Ambuye sanangolenga dziko kokha, komanso dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. “Ndipo Mulungu anati, Pakhale zowunikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku,ndi zaka; zikhale zowunikira m’thambo la kumwamba; kuti ziwunikire pa dziko la pansi; ndipo kunatero. Ndipo Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziwiri; chiwunikira chachikulu chakulamulira usana, chowunikira chaching’ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.”(Genesis 1:14-16). Izi zonse ndi ntchito za Utatu wa Mulungu, yemwe ali ndi ulamuliro pa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Dziko linalengedwa la ngwiro. Adamu ndi Hava analengedwa opanda chimo, mu chiyanjano chokwanira ndi Mulungu Mulengi wawo. Ndipo keneka Mulungu akulengeza ndi Mawu Ake ulamuliro ndi ukulu wake wa munthu pa zolengewa zina zonse zamoyo za Mulungu. “Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchulukane, mudzaze dziko la pansi, muligonjetse; mulamulire pa nsomba za m’lengalenga, ndi pa za moyo zonse zakukwawa pa dziko la pansi” (Genesis 1:28). Apa mu Mawu Olembedwa tiri ndi chokhazikika chomwe chikhazikitsa kuti ulamuliro uli wonse womwe munthu amagwiritsa ntchito mu chiyanjano ndi Mlengi wake, uyenera kukhala pa maziko a Mawu a Mulungu. Tiyeni tisayiwale izi mu mpingo wa 6. Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi. Khristu. Ngati tifunafuna kuti tigwiritse ntchito ulamuliro motsutsana ndi Mawu a Mulungu, siwudzapindula pamaso pa Mulungu, ngakhale zitawoneka ngati ukupindula kwa ka nthawi ku mawonekedwe athu. Kuwukira kotsutsa Ulamuliro wa Mulungu. Mitu yotsegulira ya buku la Genesis imalengezanso za udani ndi kutsutsa kwa Satana kotsutsa ulamuliro wa Mulungu. Pomwe mawu oyamba olankhulidwa ndi Mulungu mu Genesis ali okhudza za kupereka kwa kuwala, mawu oyamba a Satana kwa Hava ndi akuti “Eya! Kodi anatitu Mulungu?” (Genesis 3:1). Kuyambira pa chiyambi pomwe Satana amatsutsa ulamuliro wa Mulungu umamuyesa munthu kuti awukire natsutsa Mawu a Mulungu nawatsogolera anthu ku mdima wa uzimu. Pakubzyala mwa anthu chikayiko pa Mawu a Mulungu, chimagonera pa muzu wa kuwukira kutsutsana ndi Mulungu. Chiyeso ndi chakuti zambiri zingathe kupezedwa pakudya kwa chipatso choletsedwa; “mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoyipa.” (Genesis 3:5). Satana akuyesabe abambo, amayi ndi ana lero pakuwafunsa Mawu a Mulungu; “Kodi Baibulo lingathedi kutsatiridwa mu zonse zomwe tichita mu moyo wa masiku ano? Zowonadi pali njira ina yabwino yoposa kuti tiyitsatsatire? Nyengo zasintha, ndipo sikoyenera kunena kuti ndiwe wachikale popeza ukutsatira Mawu a Mulungu mosamalitsa? Ngati timakhala kuti tikuchita monga mwa zabwino kwambiri zomwe tikhumba kuchita, Mulungu sangakhudzike nazo”. Tiyeni tifufuze chisomo cha Mulungu kuti tiyankhe Satana, motsatira ndi kudalira pa Ambuye Yesu Khristu. Iye anamuyankha Satana, “Kwalembedwa, munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akuturuka m’kamwa mwa Mulungu”. (Mateyu 4:4). Sitidzakhala ndi moyo ndi ena mwa Mawu a Mulungu ndi ena a Satana. “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa Ambuye awiri.”(Mateyu 6:24). Tiyeni tkumbukire chilango choperekedwa kwa Adamu ndi Hava chifukwa cha chimo lowukira la kutsutsana ndi Mulungu ndi ulamuliro Wake. Atadya chipatso choletsedwa, maso anatseguka. Anazindikira kuti anali amaliseche ndipo anadzipangira zovala za masamba a mtengo wa mkuyu. Chophimba ichi chomwe anapanga chinali cha nthawi yochepa; sichikadakhoza kuphimba chimo lawo pamaso pa Mulungu. Adamu ndi Hava anali ndi mantha ndi kupezeka kwa Mulungu ndipo anabisala. Anathamangitsidwa kuchoka ku 7. Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi. Paradiso ndipo iwo pamodzi ndi nthaka zinatembereredwa chifukwa cha kuwukira kwawo kwa kutsutsana ndi Mulungu. Komatu, Ambuye anali nawo chifundo, nawapatsa malonjezo a mtengo wapatali a Messiah, mbewu ya mkazi (Gensis 3:15). Kuwonjezera apo, Ambuye anawawonekera iwo. “Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wake maraya azikopa, nawaveka iwo” (Genesis 3:21). Mwazi unakhetsedwa kuti Adamu ndi Hava avekedwe, zomwe zikuyimira mwa chifanizo cha mwazi wokhetsedwa wa Ambuye Yesu Khristu. Kotero kuti, Yesu yekha ndiye chiyembekezo chathu, monga tonse mwa chibadwidwe cha umunthu tiri ana amuna ndi akazi a Adamu ndiponso ochimwitsitsa pamaso pa Mulungu. Yesu Khristu anamvera Mulungu Atate mwa ngwiro ndipo anachita chilungamo kuti aphimbe ochimwa umariseche, kuti mwa Mzimu Woyera akhoze kubweretsedwa ku kulapa ndi kuwalimbikitsa ndi chikondi kuti afikitsidwe kwa Mulungu, pakukhulupirira pa Iye ndi kudandawulira pa dzina la mtengo wapatali la Yesu. Zophunzitsa za chiyambi cha dziko monga mwa kusintha kwa zinthu pakupita kwa nyengo, komanso za moyo ndi anthu zili chitsutsa cha chindunji ku ulamuliro wa Mulungu. Chimalimbana ndi kutsegulira kwenikweni kwa ndime za Mawu Olembedwa, polankhula kwa anthu ambiri kuti, “kodi anatitu Mulungu?” Sitiyenera kunyengereredwa pa nkhani ngati imeneyi. Imafunafuna kuchepetsa kusiyana komwe Mulungu anapanga pakati pa mwamuna ndi makazi, pakati pa anthu ndi nyama. Mu mitu yotsegulira ya Baibulo, Mulungu anamuyikira mwamuna ulamuliro kuti alamulire mkazi wake mu chikondi. (Genesis 3:16, Aefeso 5:22-29). Timawerenganso kuti; “ndipo Yehova Mulungu anawumba munthu ndi dothi la pansi, nawuzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wa moyo.” (Genesis 2:7). Chifukwa cha ichi, bambo aliyense, mayi ndi mwana ali osiyana ndi nyama pokhala ndi moyo womwe si umafa. Pomwe tingathe kuganiza kuti tingathe kuthawa ulamuliro wa Mulungu mu moyo uwu, tidzadziwa ndithu za ulamuliro Wake kwa muyaya, pomwe matupi athu afa ndi pomwe moyo wathu uwonekera pamaso pa Mulungu woyera kufotokoza mlandu wathu kwa Iye. Kutumikira Cholengedwa kapena Mulengi Tiyeneranso kuti tichenjeze za kuwopsya kwa kutumikira cholengedwa 8. Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi. koposa Mulengi. (Aroma 1:25). Izi zikuchuruka masiku ano ndipo zikuchitika mu njira zosiyana, osati mu dziko mokha, komanso pakati pa akhristu ovemerezeka, ngakhalenso iwo osamalitsa chikhristu chawo. Izi zimawoneka mu kukonda ndi kukundika chuma. Tiyenera kuti tifunse: kodi pali kungokhazikika pa kufunafuna chuma ndi zokondweretsa za dziko lino, ndi kukana kusiya zokoma za dziko chifukwa cha Khristu, koma pali kufunafuna kulungamitsa uzimu womwe timawona ngati ndiwotero monga a Farisi. Tiyeni nthawi zonse tikumbukire kuti Mulungu amawona kudzera mu chobisalira cha chipembedzo. Adamu ndi Hava adayesa kubisala kwa Mulungu pa zimene adachita; momwenso ndi momwe adachitira Hananiya ndi Safira. (Machitidwe a Atumwi 5:1-11). Kodi mitima yathu ndi yowumitsidwa kutsutsa ulamuliro wa Mulungu kuganiza kuti tikhoza kuti tikhoza kunyenga Mulungu, pamene ena alephera? Kulambira ndi kulemekeza cholengedwa koposa Wolenga sizimawoneka mu chipembedzo cha ochimwa a ‘New Age Movement’ komanso mu zomwe zimapanga zomwe tikhalamo. Kuwonjeza apo tiyenera kuwachenjeza Akhristu za zowopsya za kutengapo gawo popanda cholinga chiri chonse mu zinthu izi, poganiza kuti tikhoza kusewera ndi moto koma osapsya. Pali mawonedwe osiyana ambiri masiku ano mokhudzana ndi chilenegdwe chotizinga, zakudya zoyenera, njira za mapangidwe a zakudya ndi mankhwala. Sichachilendo kupeza Akhristu ovomerezeka akuyika patsogolo mawonedwe akuti chiri chonse cholengedwa chiri chabwino ndi kuti chiri chonse chopangidwa ndi munthu chiri choyipa. Poyamba, tiyenera kuchenjeza kuti izi ndi zotsutsana ndi Mawu a Mulungu. Monga tafotokoza kale m’mbuyomu, buku la Genesis likufotokoza momveka bwino kuti si munthu yekha yemwe ali otembereredwa, komanso nthaka ndi chiri chonse chomwe chitulukamo. (Genesis 3:16-19). Dziko lonse linayipitsidwa ndi chimo la munthu chifukwa cha kusamvera kwake kwa Mawu a Mulungu. Chachiwiri ndi chakuti, zambiri za zomwe anthu akuzipanga ndi kuzitsatira ziri nawo maziko mu zipembedzo za Satana kapena za matsenga, ndiye tingayembekezere kokondera kwa Mulungu bwanji, koma pokhapokha titadzipatula kwa iwo? (2 Akoronto 6:14-18). Timachita bwino tikamadziyesa tokha mosamalitsa mu zinthu izi, kuti miyoyo yathu ikhale pa maziko a Mawu a Mulungu ndi ku malemekezo ndi ulemerero wa Mulungu. Chifukwa cha ichi, tisapange chipembedzo chathu kukhala chotiyitanira kuti tibwerere ku thupi. 9. Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi. koma kuti tifunefune chisomo cha kubwerera kwa Mulungu monga mwa Mawu Ake olembedwa komanso osandulika thupi,omwe ndi Ambuye Yesu Khristu. Makamaka mu buku la Genesis, zinavumbulutsidwa kuti Mulungu ndiye Mulengi ndi kuti ali ndi ulamuliro pa chiri chonse chomwe chimachitika pa chilengedwe Chake. Komabe, mu dziko la anthu akugwa mu uchimo, chikhalidwe cha kugwa kwathu sichimawona izi. Pomwe tingathe kuzindikira m’maganizo zomwe Baibulo liphunzitsa, mitima yathu yochimwa imadzazidwa ndi udani ndi kuwukira chiphunzitso chotere. Pokhapokha titabadwanso kwatsopano mwa Mulungu Mzimu Woyera, sitingathe kulandira za chowonadi cha ukulu mphamvu ndi ulamuliro wa Mulungu. Amene akonda Mulungu zonse zithandizana kuwachitira ubwino. Kuti okhulupirira awone dzanja la mphamvu la Mulungu mu moyo wake ndi mu zokumananzo, zimatengera chikhulupiriro chopatsidwa ndi Mulungu. Poyang’ana ndi diso la umunthu timangowona chipatso cha uchimo ndi kuwukira kwa munthu mu kuchita choyipa, chiwawa, kukhumba zonyansa ndi kukonda chuma ndi mphamvu kuti zikupezeka pafupifupi ponse ponse mdziko la pansi. Komabe, mwa chikhulupiro “timadziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene ayitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.” (Aroma 8:28). Ngati mu nthawi ya chinzunzo, zowawa kapena masawutso timawona mwa chikhulupiriro kuti cholinga chachikulu choposa chiri kukwaniritsidwa ndi Mulungu, chomwe chidzathera mu chitinthozo ndi chiyanjano chamuyaya ndi Mulungu mwa Khristu Yesu. Tiyeni potero togonjere ku dzanja la chisomo cha Mulungu ndi pomwe omutsatira Iye agonjera ku Ulamuliro wa uMulungu Wake, pokumbukira “chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho” (Aefeso 2:4). Tiyeni tiwonenso kuti pamene Satana afunafuna kuchita ulamuliro, Satanayo sangathe kupyola malire omwe Mulungu wamulola. Chowonadi ichi chavumbulutsidwa mu mitu yoyamba ya buku la Yobu. Tiyeni potero titonthozedwe mkati mwa mazunzo monga Yobu, popeza mayesero owopsya awa m’manja mwa Mulungu ndi akuti atiphunzitse kuti tikhoza kudzimvera chisoni tokha kuti tilape ndi kupereka kwa Mulungu ulemu ndi ulemerero. Ndipo timawerenga, “Ndipo Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu kuposa chiyambi chake.” (Yobu 42:12). 10. MUTU 3 ULAMULIRO WA MAWU A MULUNGU. Lamulo loyera la Mulungu. Pakulemekeza iwo omwe akufunafuna mowona mtima kuti atsatire Ambuye tiyeni tiyang’ane nkhani ya J.C. Philpot pomwe analingalira za kusiya mpingo wa England pa chifukwa cha machitidwe awo osagwirizana ndi Mawu a Mulungu Olembedwa. Ngakhale kuti amayitanira mowona mtima pa Ambuye kuti amulanditse iye ndi kumutsogolera. Philpot patapita nthawi anavomereza: “Ndimayembekezera chozizwa china chake chobwera mkati chomwe akanamva mawu, kukhala ndi chitsogozo chodabwitsa ndipo pa kudalira kwa ichi, ndimadikirira pa chomwe Ambuye sanatanthawuze chimenecho kuti chimuchitikire monga mphatso. “anayenera kuti abweretsedwe ku kumvera kophweka kwa Mawu a Mulungu ndi mphamvu ya kutsutsa kwake mu chikumbu mtima chake. Philpot potero anasiya kutsata zolakwika izi ndi kumutsatira Khristu mu chikhulupiriro ndi chikondi, kuyenda mu mzimu wowona ndi wa kumvera Uthenga Wabwino. Kuyambira pachiyambi pomwe pa chilengedwe, timawererenga za mphamvu ya Mawu a Mulungu, monga momwe tawonera mu mitu ya m’mbuyomu. Pa ntchito iri yonse yakulenga Baibulo limalemba kuti “ndipo Mulungu anati,” apatu ndiko kuvumbulutsa za mphamvu ya ulamuliro ya Mawu. Yesero loyamba la Satana linali lobweretsa chikayiko pa Mawu a Mulungu; chinjoka chinati kwa Hava “kodi anatitu Mulungu?” Chimo ndi kugwa kwa munthu m’munda wa Eden kunachitika chifukwa cha kusamvera lamulo la Mulungu. Mawu Olembedwa amafotokoza kuti panadza mantha mwa munthu kutsatira kusamvera kwake. Ngati mkwiyo wa chilungamo wa Ambuye unavumbulutsidwa kwa Adamu ndi Hava, kodi tingaganize bwanji kuti tidzatha kuzembera ulamuliro Mawu wa Mulungu? Lamulo la Mulungu loperekedwa kwa munthu lomwe linalembedwa ndilo Mawu a Mulungu Olemebdwa kudzera mwa mneneri Mose, liri muyeso wokwanira wa zomwe ziri zonama. Tiri ndi tanthawuzo “chimo ndilo kusayeruzika.” ( 1 Yohane 3:4 ). Pamene tingathe kupanga zifukwa 11. Ulamuliro wa Mawu a Mulungu. m’mawonekedwe a munthu ndi kutsutsa kuchokera mwa ife eni kapena kunja kwa miyoyo yathu zomwe timalepherera kuchitira chiweruzo changwiro cha Mulungu, komatu pamaso pa Mulungu sipangakhale kufunsa za lamulolo, popeza liri la ulamuliro wa Mulungu. Mawu a Mulungu ayenera kuyima, chimo ndilo kuphwanya kwa lamulo, ndipo liyenera kulandira imfa yamuyaya. A Israeli pa phiri la Sinai anapatsidwa lamulo la Mulungu, iwo sanachedwe kutembenukira ku kupembedza fano. Mose anali atangolandira magome a malamulo, pomwe a Israeli anali kuvina pamaso pa mwana wa ng’ombe wa golide (Eksodo 32). Anali ndi ma umboni wokwaniriratu a mphamvu ya Mulungu ndi nyonga pamaso pawo, komabe mtima wa umunthu wa munthu wochimwa unali pa udani ndi Mulungu. Mitima yawo inadana ndi njira yowawa ndi yamayesero, ndipo anafuna kuti apeze njira ina yophweka; ndipo mitima yathu sikusiyana ndi yawoyo. Mtima wa munthu wokhala monga mwa umunthu sunasinthike kukhala wabwinopo mwa njira ina iri yonse kuyambira kuchimwa kwa Adamu, siwunasinthikenso kuchitapo bwino ngakhale kuyambira nthawi yomwe fano la mwana wa ng’ombe wa gilode linayengedwa pa phiri la Sinai. “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuwudziwa?” (Yeremiya 17:9). Tikukhala mu tsiku lomwe chikhalidwe chimafananizidwa, kapena kusiyanitsidwa. Mulingo wa Baibulo wa zomwe ziri zowona ndi zolakwika umayikidwa pambali, ambiri ndi kumasangalala kuti amphwanya gori lakale lomwe silingagwirenso ntchito lero komanso chipembedzo chakale chosagwirizana ndi chikhalidwe cha masiku ano. M’malo mwake ayikapo mulingo wosunthika wa chiri chonse cha zomwe ambiri azivomereza ndi kuzilandira. Apa, zomwe ziri zolakwika lero zingathe kukhala zolakwika mawa, ngati anthu okwanira asintha maweruzidwe awo pa kusinthako. Komabe, “Mawu a Mulungu akhala chikhalire.“ (1 Petro 1:25). Kugwirizana kwa anthu ochimwa kutsutsa Mawu a Mulungu, sikungapangitse kuti Mawu a Mulungu akhale opanda mphamvu. Dziko losapembedza Mulunguli limawonetsa udani kutsutsa ulamuliro wa Mulungu mwa kuwukira poyera ndi kusasamalira kwa Mawu a Mulungu; koma nanga kwa iwo omwe ali Akhristu ovomerezeka? Mu mpingo muli kuwukira kotichenjerera kopitirira komanso kutsimikizika koposa kotsutsa 12. Ulamuliro wa Mawu a MUlungu. ulamuliro wa Mawu a Mulungu. Ena akutsogozedwa ndi chikhalidwe cha moyo wa masiku ano, ena ndi miyambo ya kale. Mpingo kapena utumiki ungathe kusankhidwa chifukwa uli wotchuka kapena amasonkhana anthu ambiri, m’malo mwa “kusankhula kuchitidwa zoyipa pamodzi ndi anthu a Mulungu.” (Ahebri 11:25). Pali kufufuza kwa Mawu Olembedwa kochepa, changu cha pa chowonadi cha Mulungu chochepa, palibe kuyamikira kwa ulemerero wa Mulungu, palibe kukhumba kwa kuwoneka osiyana ndi ena a mamembala a mu mpingo omwe amalingalira za dziko la pansi. Kuwukira uku kungathe kuwonekeranso mwa kukakamira ku miyambo, ya banja kapena ya mpingo. Mayitanidwe ena ali wonse kapena lamulo la m’Baibulo lomwe lingawayike kunja kwa momwe ziyenera kukhalira amalipewa, ngakhale kuti liri Mawu omveka bwino a Mawu a Mulungu. Kutakhala kuti “tiyenera kulindira pa Ambuye”, kapena “sitikutsogozedwa ndi Mzimu za ichi”, ndipo pa nthawi ino zokoma za dziko la pansi zikukondwereredwa kwathunthu ngati machitidwe a chipembedzo avomera. Mu zenizeni, izi ndi zowonekera poyera ndi kufuna dala kwa kusamvera kwa ulamuliro wa Mulungu. Mphamvu ya Uthenga Wabwino. Monga momwe Mawu a Mulungu alengeza za uthunthu wa mulingo wa kukhoza ndi kulakwa, momwenso alengeza za njira ya chipulumutso kudzera mwa Yesu Khristu ndi ulamuliro womwewo. Mawu Olembedwa amakhazikitsa uMulungu Wake, umunthu Wake wa chiyero, kumvera kwa ngwiro Kwake ku lamulo loyera la Mulungu ndi imfa yake ngati mwana wa nkhosa wa Mulungu, kupereka nsembe ya ngwiro ya machimo a Mpingo wowona wa Mulungu pa mtanda, ndipo kenaka kuwukanso kuchokera ku imfa kuti tikhoze kukhala ndi moyo mwa Iye. Chowonadi chokha mwa Yesu Khristu, Mawu a Mulungu a muyaya, ndi chomwe chimamasula ochimwa otsutsidwa pansi pa lamulo la Mulungu (kuphatikizapo ochimwa achipembedzo) kuwachotsa ku ukapolo wa chimo, imfa ndi gahena. Ambuye anati, “Ngati mukhala inu m’mawu anga muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira chowonadi ndipo chidzakumasulani.”(Yohane 8:31-32). Iyi ndi ntchito yodalitsika ya Mulungu Mzimu Woyera kutsogolera ku chowonadi chonse. (Yohane 16:13). Apatu tiyenera kukhala mu moyo wopemphera kwambairi kuti Mzimu athe kutitsogolera, kutikoka ndi kuchita Mawu a Mulungu. Sangalephere 13. Ulamuliro wa Mawu a Mulungu. kuthandiza wochimwa wosawuka yemwe adzipereka yekha ku kuchita lamulo lake. Tisowa kumasulidwa ndi Mzimu Woyera kuchoka ku mzimu wonyansa womwe umanong’oneza kuti “aunyinji ayenera kukhala wokhoza” ndi chiwanda cha mtundu wake womwewo chomwe chimati “muyenera kusamalira miyambo yathu.” Koma ife tiyenera kunena kuti, “Mulungu akhale owona, ndipo anthu onse akhale onama.” (Aroma 3:4). Tiyeni tipemphere kuti tidzazidwe ndi changu cha pa Mawu a Mulungu, chowonadi chake, ulemerero Wake, ndi kugonjera mokondwera ku ulamuliro Wake. Mawu a Mulungu amalengeza ndi ulamuliro momwe Mpingo uyenera kuyendetsedwera komanso za moyo wa wokhulupirira aliyense. Komabe izi siziri monga mwa mphamvu za ulamuliro. Mphamvu zimadzera ku ntchito zodalitsika za Mzimu Woyera. “Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu onse. Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m’kati mwanu mzimu watsopano, ndipo ndidzachotsa mtima wa mwala m’thupi, ndi kukupatsani mtima wa mnofu. Ndipo ndidzayika mzimu wanga m’kati mwanu, ndi kukuyendetsani m’malemba anga ndi kuwachita” (Ezekiel 36:25-27). Ndiye kuti, ulamuliro ndi mphamvu za Mawu a Mulungu pa wokhulupirira zimachitika ndi kukakamiza kokoma kwa Mzimu kuvumbulutsa chikondi chotifera cha Khristu. Kawiri mu makalata omwe atumwi analembera mipingo mu Baibulo, wolemba wodzozedwa amatifikitsa pa “kulingalira Iye.” (Ahebri 12:3) kuti “tikhale nawo mtima mkati mwathu umene unalinso mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 2:5), potikumbutsa za chikondi cha Mulungu chowonetsedwa mwa Yesu Khristu. Kudzera mu mphamvu ya kuwuka kwake kwa Khristu ndi momwe tikhala ndi moyo ndi kutumikira Mulungu mu moyo watsopano, ndi kubereka zipatso zopereka ulemerero wa Mulungu kuyenda kudzera mu chiyanjano cha uzimu ndi Khristu (Yohane 15). “Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza” (2 Akoronto 5:14). Lalikira Mawu. Talankhula za mamembala a pa mpingo, nanga wolalikira bwanji? Kodi chitsogozo ndi chiphunzitso amazifunafuna kuti? Kodi ndi kuchokera ku wailesi ya kanema, kapena ku uthenga wojambulidwa womwe akuwonera 14. Ulamuliro wa Mawu a Mulungu. wina akulalikira? Kapena amatenga zophunzitsa kuchokera ku zomwe anaphunzira ku sukulu ya Mawu a Mulungu (Ya Ubusa)? Kodi wolalikira akungofuna kutengera ena omwe akuchita bwino ndi kuti anthu amuyamikire.” Komabe, mtumwi Paulo analengeza, “Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu.” (Agalatiya 1:10). Mlaliki wa Uthenga Wabwino ayenera kulengeza “uphungu wonse wa Mulungu”. (Machitidwe a Atumwi 20:27). Uphungu wa Mulungu umavumbulutsidwa kwa munthu mu Mawu a Mulungu owuziridwa omwe apatsidwa kwa ife mu Buku Lopatulika, liwu liri lonse linawuziridwa ndi Mulungu ndipo liri ndi ulamuliro. (2 Timoteo 3:14-17). Kudzera mu Mawu a Mulungu Olembedwa ndi momwe timakhala ndi vumbulutso lathunthu la Mulungu, maweruzo Ake ndi njira Yake ya chipulumutso mwa Khristu Yesu. Chifukwa cha ichi Paulo anamulimbikitsa Timoteo kuti, “Lalika mawu” ndi kuti “Uchite changu kudziwonetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wa ntchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi wolunjika nawo bwino mawu a chowonadi.” (2 Timoteo 4:2, 2:15). Kulalikira kwa Mawu a Mulungu uku sikuyenera kukhala mwa njira iri yonse ya chiphunzitso chowuma, kapena mu chidziwitso cha kuphunzira, koma kuchokera mu kulengeza kokhulupirika kwa Mawu a Mulungu pamodzi kudzoza kwa Mzimu Woyera, “Pakuti Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m’mawu mokha, komanso mu mphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera ndi m’kuchuruka kwakukuru.” (1 Atesalonika 1:3). Mtumiki wolalika Uthenga Wabwino ayenera kukhala mboni ya zomwe iye akudziwa monga munthu yemwe ali pansi pa ulamuliro wa uMulungu. Mtumiki Yohane analengeza mwa kudzozedwa kwa Mulungu, “Chimene chinaliko kuyambira pa chiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachipenyerera, ndipo manja anthu adachigwira cha mawu a Moyo, (ndipo moyowo unawonekera, ndipo tidawona, ndipo tichita umboni, ndipo tikulakirani moyo wosathawo, umene unali kwa Atate, nuwonekera kwa ife); chimene tidachiwona, ndipo tidachimva tikulakirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife, ndipo chiyanjano chathu chirinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu.” (1 Yohane 1:1-3). Kulephera apo, sipadzakhala ulamuliro wa uzimu mu utumiki. Anthu angathe kuyesera zomwe zimakondweretsa kuti akole ku kugwiritsa ntchito mphamvu zawo pa 15. Ulamuliro wa Mawu a Mulungu. anthu afowoka, kuti akakamize kapena kugometsa, kutenga mwa kutamandira, koma mtumiki yemwe amagwiritsa ntchito njira za ku thupi kuti awonetse ulamuliro wake pa anthu kapena kuti mpingo wake ukule mu chiwerengero (ngakhale atakhala kuti akuwoneka kuti akupambana pamaso pa anthu) iye ali mu kuwukira kotsutsa ulamuliro wa Mawu a Mulungu. Gwiritsitsani Mawu Okhulupirika a Chowonadi. Okhulupirira owona ndiponso enieni amasocheretsedwa ndi kuti mipukutu ina yakale (yomwe inakanidwa ndi mipingo pakupita pa nyengo kuti ndiyosadalirika) iyenera kugwiritsidwa ntchito tsopano pomanganso Mawu Olembedwa ndi kuti azigwiritsidwa ntchito. Njira imodzi yalutha yomwe Satana akuyigwiritsa ntchito mu mibadwo yatsopano ndiyo kubweretsa Mawu a Mulungu olembedwa omwe ali otanthuwuzidwa molakwitsa. Izi zimakopa mwamitundu yisiyana kwa chikhumbo cha munthu wakugwa cha mabuku wamba ndi njira zomwe ambiri azitsatira za matanthawuzidwe a Baibulo. Kawirikawiri zolinga zawo posindikiza bodza lawo zimakhala mwa zokhumba za wosindikiza kuti apeze phindu lalikulu kwa Akhristu okhala mwa umunthu, kapena kuchokera mu zolakwitsa kapena ophunzira a Mawu a Mulungu omwe akupititsa patsogolo mphekesera chabe. Pofunafuna kuti akhazikitse zikhulupiriro zawo pa mipingo. Kulephera apo, matanthawuzidwe ena amachokera mu mawonekedwe osatsogozedwa, akuti zowonadi za uzimu zingathe kuphunzitsidwa mwa kuphweketsa chilankhulo choperekedwa ndi kuwuziridwa ndi Mulungu. Munthu akapita ku nyumba yogulitsa mabuku angathe kupezako mitundu yambiri ya matanthawuzidwe a Baibulo, onsewo kumatsimikizidwa kuti ndi Mawu a Mulungu, komatu mu malo ambiri samagwirizana lina ndi linzake. Ambiri a iwo ali mboni zonama zomwe zikufesa chisokonezo pakati pa mipingo ndi okhulupirira osakhazikika omwe sangazindikire bwino lomwe kuti Mawu a Mulungu eni eni ndi ati. Woyambitsa chisokonezo chotere si Mulungu, koma Satana yemwe kuyambira mu Eden wakhala akufunafuna kuti anong’oneze kuti. “kodi anatitu Mulungu?” Chotsatira chotsiriza ndicho zomwe tichitira umboni lero, pomwe wowerenga akusiyidwa pa malo akuti asankhe matanthawuzidwe omwe iye akukonda kwambiri, osati kuti agwe 16. Ulamuliro wa Mawu a Mulungu. modzichepetsa pansi pa ulamuliro ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu. Zokhotetsa za masiku anozi zachepetsa ulamuliro wa Mawu mu mitima ndi miyoyo ya Akhristu ovomerezeka ambiri. Zikadakhala zochitika bwino kupitirira cholinga kuchikwaniritsa mu buku laling’ono ili, kuti tilowe mu kukambirana za matanthawizidwe asiyana siyana a Baibulo. Komabe, mu chilankhulo cha chingerezi, Baibulo la ‘King James Version’ lomwe linatanthawuzidwa mu chaka cha 1611, ndilo lotanthawuzidwa mokhulupirika kwambiri lomwe lisunga Malembo a mipukutu yomwe inali yoyambirira kulembedwa, lomwe linatanthawuzidwa ndi anthu akhulupirika ndi a uzimu; kusonyeza kuti mu chingerezi limalandiridwa ngati Mawu a Mulungu olembedwa. Ziri zofunika ku mbali ya moyo wa uzimu wa mipingo kuti Mawu a Mulungu osadetsereredwa akugwiritsidwa ntchito, kuwerengedwa. Komabe, tiyeni tichenjezedwe kuti mwina tingagwiritse ntchito Baibulo lotanthawuzidwa mokhulupirika la Mawu a Mulungu, koma ndi kusakhulupirika mu njira yomwe tikuwagwiritsira ntchito Mawu Olembedwawo. Kodi tikuwamasulira Mawu Olembedwa monga mwa miyambo yathu? Ndiye kuti Mawu a Mulungu ali kupereka ulemu ku miyambo yathu ndi kuti tiri mu chiyanjano ndi Afarisi, osati Mwana wa Mulungu. Nthawi iri yonse yomwe sitizindikira Mawu Olembedwa tiyeni titsatire ndondomeko ya uMulungu yomwe Mawu Olembedwa amamasulidwira. Monga Mulungu Mzimu Woyera anawuzira Mawu Olembedwa a Mullungu, kodi Mzimuyo sadzavumbulutsira chowonadi kwa okhulupirira odzichepetsa omwe afunafuna kuwunika ndi chitsogozo mwa pemphero? (Luka 11:13). Tiyeni tipemphere kuti Mulungu Mzimu Woyera atsegule mitima yathu kuti tilandire Mawu ndi kutipatsa mphamvu kuti tiyende mu mawuwo. Pali kusowekera kwakulu mu mpingo masiku ano kwa pemphero lowona la munthu, kuwerenga ndi kufunafuna Mawu. Ngakhale pali zolimbana ndi ulamuliro wa Mulungu wa Mawu a Mulungu. Malonjezo a Muluggnu ndi okhazikika, “Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko la pansi ndi chiyikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti? Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinawoneka, Ati Yehova; koma ndidzayang’anira munthu uyu amene ali wa 17. Ulamuliro wa Mawu a Mulungu. umphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mawu anga.” (Yesaya 66:1-2). MUTU 4 ULAMULIRO WA KHRISTU MONGA MUTU WA MPINGO. Kuwukanso kwa Akufa. Talingalira za ulamuliro wa Mawu a Mulungu Olembedwa, ndipo tsopano tiyenera tilingalire za ulamuliro pa mpingo wa Ambuye Yesu Khristu, Mawu osandulika thupi. (Yohane 1:1-14). Ambuye Yesu Khristu, pakuyamba pa utumiki wake wa dziko la pansi, anabwera ku Yerusalemu ndi kolowa mu Kachisi. Mmenemo anapeza ogula, ogulitsa ndi osintha ndalama amitundu yosiyana siyana. Mu mkwiyo wake wolungama anayeretsa mpingo ku zinthu zoterezi. “Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anaturutsa onse m’Kachisimo, ndi nkhosa ndi ng’ombe; nakhuthula ndalama za osinthawo, nagubuduza magome, nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.” (Yohane 2:15-16). Ayuda ndipo anafuna kuti Yesu apereke chizindikiro cha ulamuliro Wake wakuchitira zinthu zotere. Yesu anayankha , “Gwetsani Kachisi uyu, ndipo ndidzamumanganso mu masiku atatu.” Yesu amalankhula za kachisi wa thupi Lake, kulengeza za chitsimikizo cha ulamuliro wake pa mpingo kuti unayenera kukhala imfa Yake ndi kuwukanso kwa akufa. Kuwonjezera apo, kuwukanso kwa akufa kwa Yesu Khristu kuli chitsimikizo chakuti ali Mwana wa Mulungu. Paulo analemba kuti Iye amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa Chiyero, ndi kuwuka kwa akufa.” (Aroma 1:4). Ayuda a chipembedzo sakadakhoza kulandira kapena kukhulupirira izi, ngakhale kuti mwachangu ndi khama amalondoloza miyambo yawo ya chipembedzo. Koposatu makamaka kwa Ayuda osakhulupirira, koma kodi tiri ndi makutu kuti “timve chomwe Mzimu alankhula ku mipingo?” (Chivumbulutso 2:29). Ambuye Yesu Khristu wowuka kwa akufa ndi wopatsidwa ulemerero anawonekera kwa mtumwi Yohane pa chisumbu cha Patmo ndi kulengeza ndi 18. Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo. ulamuliro za chiweruzo chake changwiro pa mipingo isanu ndi iwiri ku mipingo ya ku Asia. Zinthu izi zinalembedwa kuti zitilangize ndi kutichenjeza, ndipo mipingo siyidzathawa ziweruzo zolungama za Mutu wamkulu wa Mpingo pokhapokha ngati tilandira ndi kumvera chilimbikitso chochokera kwa Khristu mwini, “potero chita changu, nutembenuke mtima.” (Chivumbulutso 3:19). Paulo anachenjeza mpingo wa ku Ahebri; “Penyani musakane wolankhulayo.” (Ahebri 12:25). Mtumwi Paulo akulembanso kwa Aefeso za mapemphero ake owona mtima kuti apatsidwe nzeru, chidziwitso ndi kuzindikira kwa “chiyembekezo cha kuyitana kwake nchiyani, chiyaninso chuma cha ulememrero wa cholowa chake mwa oyera mtima, ndi chiyani ukuru woposa wa mphamvu yake ya kwa ife a mphamvu yake yolimba, imene anachititsa mwa Khristu, m’mene anamuwukitsa kwa akufa, namkhazikitsa pa dzanja lake la manja m’zakumwamba, pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina liri lonse lotchedwa, si m’nyengo yino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza; ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamtu pa zonse, kwa Eklesia amene ali thupi lake, mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse mu zonse.” (Aefeso 1:18-23). Chikhululukiro cha Machimo. Tikapitirirabe kuwerenga kalata ya Paulo yolembera mpingo wa ku Efeso, timawona kuti, “Khristu ndiye mutu wa Eklesia; ali yekha Mpulumnmutsi wa thupilo” (Aefeso 5:23). Khristu monga Mutu wa Mpingo ali nawo ulamuliro ndi mphamvu kukhululukira chimo. Pomwe adabweretsa kwa Yesu munthu yemwe ankadwala matenda a manjenje, amene mwa chikhulupiriro adamugoneka pa mapazi a Yesu, Ambuye anati “Mwana, machimo ako akhululukidwa. Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mu mitima mwawo, Munthu amene atero bwanji? Achita mwano; akhoza ndani kukhululukira machimo koma m’modzi; ndiye Mulungu?” (Marko 2:5-7). Keneka Yesu anawonetsera mwa kuchiritsa mozizwitsa munthu ameneyu, kuti Ali nayo mphamvu pa dziko ya kukhulukira machimo ndi kuti Iye zowonadi ali Mulungu wowonetsedwa mu thupi (1 Timoteo 3:16). Zowonadi zake ndi zakuti Yesu Khristu ndi Mulungu, Mfumu ya Mafumu ndiponso Ambuye wa Ambuye. Mwa chisomo Iye amachitachita mwa 19. Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo. mphamvu imeneyi ndi ulamuliro umenewu, monga Mutu wa Mpingo, kuti awombole ochimwa kudzera mu mwazi Wake wa mtengo wapatali. Okhulupirira owona mtima ali ogulidwa ake. “Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m’thupi lanu,’ (1 Akorinto 6:19-20). Izi zimalankhula za ntchito ya Khristu ya chiwombolo kudzera mu mwazi wake wokhetsedwa kuti apulumutse ochimwa, kuwabweretsa iwo kwa Iye kudzera mu ntchito yodalitsika ya Mzimu Woyera ndi kuti awasunge mu chikondi pansi pa ulamuliro Wake. A Yuda osakhulupirira, sanamvere Uthenga Wabwino, koma anali osamvera ku mawu ndi ntchito ya Ambuye Yesu Khristu (Aroma 10:16). Ngakhale kuti “Anawaphunzitsa monga mwini mphamvu.” (Mateyu 7:29), anapitirirabe kudzilungamitsa okha pansi pa chilamulo. Mtumwi Paulo analemba za momwe Ambuye anamumasulira Iye (Khristu), wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m’lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro.” (Afilipi 3:9). Chipulumutso sitimachipeza kudzera mumphamvu yathu ndi ufulu wakusankha, “koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwotu anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu akukhulupirira dzina lake; amene sanabadwwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.” (Yohane 1 :12-13). Mu ndime iyi ya Mawu Olembedwa mawu ayambirira omwe anatanthawuzidwa “mphamvu”. Omwe tawonanso m’mbuyomu kuti akutanthawuzanso “ufulu” kapena “mwayi”. Apatu ndiye kuti ndi kuchokera kwa Khristu Mutu wa Mpingo yemwe anakwaniritsa lamulo loyera la Mulungu, kuti wochimwa wobwera kwa Yesu amapatsidwa mphamvu ndi mwayi mwa Mzimu Woyera kudzera mu chikhulupiriro kuti angathe kufikira chipulumutso chachikuru chotere. Izi zikuwoneka kuti zikufanizidwa ndi nkhani ya Yakobo kulandira dalitso pa doko la Yaboki, “ndipo analimbana naye munthu kufikira mbandakucha. Ndipo pamene anawona kuti sanamlaka, anakhudza nsukunyu ya ntchafu yake; ndipo nsukunyu ya ntchafu yake ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye. Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kuli kucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa 20. Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo. ine. Ndipo iye anati kwa Yakobo. Dzina lako ndani? Nati iye, Yakobo. Ndipo nati dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israeli, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.” (Genesis 32:24-28). Mwa manyazi tiyenera kuyang’ana kuchepa kwa mapamphero opambanitsa omwe akuchitika mu masiku ano, kaya ndi pa gulu ngakhale mwa mseri. Kawirikawiri mu Mawu Olembedwa timawerenga za ulamuliro ndi mphamvu za mapemphero a aneneri, monga Mose, Eliya ndi Elisha. Mphamvu imeneyi simachokera mwa iwo eni, koma kwa Mulungu. Ambuye Yesu Khristu akuvumbulutsa chinsinsi cha pemphero. “Ngati mudzapempha Atate kanthu adzakupatsani inu m’dzina langa” (Yohane 16:23). Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mudzati ndi phiri iri, senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo kulibe kanthu kadzakulakani kosachitika.” (Mateyu 17:20) “Ndipo pamene Iye anadziyitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu (Ulamuliro) pa mizimu yoyipa, yakuyiturutsa, ndi yakuchiza nthenda iri yonse ndi zofoka zonse.” (Mateyu 10:1). Tikubwerezanso kunena kuti mphamvu ndi ulamuliro uwu zimachokera kwa Khristu, inde Khristu yekha basi, ndipo imadziwidwa pomwe titsatira mayitanidwe a uMulungu wake. Mphamvu iyi singapezeke mwa njira ina iri yonse ngakhale kugulidwa ndi ndalama. (Machitidwe a Atumwi 8:18-21). Tiyeni mowona mtima tidandawulire Ambuye kuti mwa chisomo atipatse mzimu wowona wa pemphero la kulimbana ndi kuwonjezera kwa chikhulupiriro monga mu masiku otsiriza timapempherera zinthu zomwe zavumbulutsidwa bwino lomwe mu Mawu a Mulungu. Ulamuliro pa Mpingo. Monga Ambuye Yesu Khristu ali Mutu wa Mpingo, kotero ali ndi ulamuliro wa uMulungu pa miyoyo ndi mayitanidwe kuyambira a mpingo komanso wokhulupirira ali yense pa yekha omwe amapanga mpingo. Ali ndi ulamuliro kuyitana ndi kutsogolera monga Iye afuna; koma palibe kuyitana kapena kutsogozedwa ndi Mulungu komwe kungakhale kotsutsana ndi Mawu a Mulungu owuziridwa Olembedwa. Sipadzakhala kusiyana pakati pa chitsogozo cha Mzimu Woyera ndi Mawu a Mulungu Olembedwa ndi osandulika thupi; ndipo mu zinthu zonse Mzimu ndi Mawu zinakwaniritsa zolinga za muyaya za Atate. “Pakuti pali atatu akuchita umboni, Mzimu, ndi 21. Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo madzi, ndi mwazi, ndipo iwo atatu ali m’modzi.” (1 Yohane 5:8). Tisowa kudzichepetsa ndi kugonjera, kulindira pa kuyitana kwa Ambuye; ndipo pomwe kwalandiridwa, tisowekeranso kwambiri kuti timvere ndi kuyenda mu mayitanidwewo. Zingathe kukhala kuti mayitanidwe omwe takhala tikuwafunafuna, kapena njira yomwe takhala tikuyilingalira. “Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu siziri njira zanga, ati Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutari ndi dziko la pansi, momwenso njira zanga ziri zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.” (Yesaya 55:8-9). Kapena siyidzakhala njira yophweka “tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisawutso zambiri” (Machitidwe a Atumwi 14:22). “ndipo onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo.” ( 2Timoteo 3:12). Koma ndi njira yomwe imatitengera ku moyo wosatha. Ali ndi mphamvu ndi ulamuliro kuti atisamalire ife kuchokera kwa adani athu onse, kuchokera ku chimo, chiwonongeko, imfa ndi gahena. Adzatipyoletsa mayesero athu onse. Pamene anthu a Ambuye apatuka pa njira ya chowonadi, kaya ndi mu kusamvera, kunyada, kusasamala, kapena kupereka ulemu ku miyambo ya makolo athu, Ambuye ali ndi ulamuliro wa uMulungu kuti apereke chilango. Komatu kupereka mwambo uku kumachitidwa mu chikondi ndipo ku ubwino wa ife, ndiponso chiri chikole cha chikondi chake. Pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, kulanga uku ndi “kukatipindulitsa, kuti tikalandire nawo pa chiyero chake. Chilango chiri chonse pakuchitika, sichimamveka chokondweretsa, komatu chowawa, koma chitatha, chipereka chipatso chamtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. Mwa ichi limbikitsani manja ofowoka, ndi mawondo olobodoka, ndipo lambulani misewu yolunjika yoyendamo mapazi anu.” (Ahebri 12:6-12). Utumiki wa Wukulu wa Kulalikira. Atawuka kwa akufa Ambuye, chomwe chiri chitsimikizo chachukulu cha ulamuliro wa uMulungu wake, Ambuye anawonekera kwa akuphunzira ake. Analankhuila mawu achitonthozo ndi mtendere; ndipo izi zinadza ndi mphamvu mu mitima yawo. Ndipo anawapatsa ntchito yomwe imadziwika kuti Utumiki Wawukulu yakulalikira Uthenga Wabwino. “Mukani ku dziko lonse la pansi lalikirani Uthenga Wabwino kwa olenegdwa onse.” (Marko 22. Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo. 16:15). Ku Mateyu 28 kunalembedwanso kuti Ambuye anatuma ophunzira Ake kuti “aphunzitse anthu a mitundu yonse” ndi ku Machitidwe a Atumwi mutu woyamba, Ambuye atawuka kwa akufa anati, “mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera atadza pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko la pansi” (Machitidwe a Atumwi 1:8). Polingalira za Utumiki Wawukulu, ziphunzitso zathu zonse ziyenera kukhala pa maziko a Mawu Olembedwa; osawonjezepo kena kali konse kapena kuchotsa pa Mawu a Mulungu. Pomwe pali kuyenera kutsindika kuti palibe munthu yemwe angathe kulalikira mowona kapena molunjika, pokhapokha ngati watumidwa ndi Mulungu (Aroma 10:15), ndi mayitanidwe a mipingo yonse pamodzi komanso okhulupurira ali yense payekha payekha kuti akhale mboni za Khristu mu tsiku la mdima ndi loyipa. Tiyeni tifunefune chisomo cha Mulungu kuti tichite motero mu mzimu wowona wa chikondi, mwawuthunthu kutsatira Mawu a Mulungu. Pomaliza, tiyeneranso kuwona kuti pali kusiyana pakati pa Utumiki Wawukulu ndi zizindikiro zomwe Ambuye analonjeza kuti zidzatsatira malingana ndi chifuniro chake cha uMulungu. Pomwe membela wokondedwa kapena mlaliki akufuna kuti anyamuke kuchoka pa mpingo, angathe kupereka mawu a malangizo otsanzikana, kapena amakhala mawu awo omaliza. Kufunika kwakukulu kumaphatikizidwa ku mawu otere, ndipo mamembala a tchalitchi kawirikawiri amakumbutsidwa patapita nthawi za uphungu wa woyera mtima, yemwe wachoka. Ngati zinthu zimakhala choncho, ndi chifukwa chiyani pali kupereka ulemu kochepa ku mawu otsiriza a Yesu Khristu, amene ali Mutu wa Mpingo? Tisanazilingalire moposera izi, tiyeni tiwerenge nkhani yathunthu ya Utumiki Wawukulu womwe unaperekedwa mu Uthenga Wabwino wa Mateyu. “Ndipo Yesu analankhula nawo, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko la pansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi Mzimu Woyera; ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu, ndipo onani Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 28:18-20). Njira yomwe inalembedwa mu Mawu a Mulungu yomwe ndi yotumizira kwa anthu njira ya chipulumutso simangophatikiza ku kulakira, komanso Mawu a Mulungu Olembedwa (Yohane 20:31) pamodzi ndi umboni wa munthu payekha. Kuchokera ku 23. Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo. Mateyu 28, timawona chifukwa chake chenicheni cho “mukira ku dziko lonse la pansi ndi kuphunzitsa anthu a mitundu yonse” kuti zigonera mu mphamvu ndi ulamuliro wa Khristu; ndi kuti mu kumuka monga mwa lamulo lake. Iye amatipatsa lonjezo lodalitsika la kupezeka Kwake kufikira ku mapeto a nthawi. Komabe, ena amapanga chiphunzitso cha umwini mphamvu wa Mulungu mu chipulumutso kudzilungamitsa kwawo pa kusasamalira za Utumuki Wawukulu, posinkhasinkha kuti chipulumutso ndi cha Mulungu ndi kuti sikuli kwa munthu kuti akhoza kuyika dzanja lake mu nkhani iyi. Koma pomwe Mulungu Mzimu Woyera akutsogolera tidzapangidwa kugonjera ndi kumvera pomutsogolera ku mayitanidwe a Mawu a Mulungu. Ubale, mphamvu ndi ulamuliro wa Khristu ziri zifukwa zenizeni zotipangitsa kumvera Utumiki Wawukulu. “Pakuti mawu a mfumu ali ndi mphamvu ndipo ndani anganene kwa Iye, Kodi uchita chiyani? (Mlaliki 8:4). Tiyeni tisamale pa kusamvetsa chisoni Mzimuyo kudzera mu kusamvera. Ena amawona kulakwitsa kwa Utumiki Wawukulu, ndi kudzibweza kuchoka ku malingaliro a “ntchito ya umishonale.” Komabe, Utumiki Wawukulu siwa kwa anthu a mitundu yonse okha, komatu kwakukulu imayenera kulalikira kokhulupirika pamodzi ndi kuphunzitsa kwa “zinthu zonse zomwe ndinakulamulirani; kulankhula mwa mawu ena, uphungu wonse wa Mulungu wovumbulutsidwa mu Mawu a Mulungu ngati tingalalikira kapena kuphunzitsa gawo la uphungu wa Mulungu wa kwa anthu a mitundu yonse, makamakatu uku ndi kuwupotoza uphunguwo. Sizirinso gawo la Utumiki Wawukulu kugwiritsa ntchito zisudzo, masewero, ziwonetsero za zidole, ziwonetsero za nyimbo, ndi zina zambiri. Sizirinso za Mawu Olembedwa kuti mowona ndi mosaledzera “kupereka” Uthenga Wabwino, ngati zaperekedwa kwa omvera kuti iwo okha ali ndi mphamvu mwa iwo okha kuti apulumutsidwe. Mawu Olembedwa amanena momveka bwino kuti “Lalikira Uthenga Wabwino.” Anthu angathe kutchula kulalikira “chopusa”, koma Mtumwi Paulo analemba: “pakuti popeza mnzeru ya Mulungu dziko la pansi, mwa nzeru yake, silinadziwa Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira. Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Ahelene atsata nzeru, koma ife tilakira Khristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa amitundu chinthu chopusa.” (1 Akorinto 1:21-23). 24. Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo. Mfundo zotsatira za zomwe tangolankhula zokhudza kulakira ziyenera kugwiritsidwa ntchito chimodzimodzi ku magawo ena a Utumiki Wawukulu, zomwe ziri kuphunzitsa ndi kuchitira umboni. Ziyeneranso kutengedwa chimodzimodzinso malingana ndi ndondomeko monga mwa Mawu Olembedwa osati monga mwa dziko la pansi. Tiyeninso tifotokozere momwe Mulungu amalemekezeredwa malingana ndi Utumiki Wawukulu mwa umboni wa okhulupirira, omwe ngakhale sanayitanidwe kuti alalikire pagulu, amachitira umboni za mphamvu ya Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu kudzera mu ntchito za chikondi. Tiri ndi zitsanzo zomwe ziri mu Mawu Olembedwa. Mwa chitsanzo pali Dorika, yemwe ankasamalira mu njira zambiri amayi amasiye. (Machitidwe 9:39); tiri ndi Gayo yemwe anali nazo ntchito za chikondi ndi kulandira ndi kusamalira alendo (3 Yohane 1-6); ndiponso pali Febe “ndiye mtumiki wa mkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkreya; kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m’zinthu ziri zonse adzazifuna kwa inu, pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe. Mulankhule Priska ndi Akula, antchito anzanga mwa Khristu Yesu. (Aroma 16:1-3). Mu tsiku la zokhumudwitsa zambiri, ena amawona kuchepa kwa anthu m’mipingo ndi kutsekedwa kwa mipingo kukhala chinthu chomwe sitingathe kuchipewa, chifukwa masomphenya a Utumiki Wawukulu atayidwa. Izi ndi zochitika zomwe zimachitika mobwerezabwereza, chifukwa Mawu a Mulungu amanena kuti, “Popanda chivumbulutso anthu amasawuka.”(Miyambo 29:18). Fanizo la ndalama zomwe zinaperekedwa kwa antchito (Luka 19:1127) limafotokoza za momwe Mbuye analamulira aliyense wa iwo “Chita nazoni malonda kufikira ndidzabweranso.” Mbuye atabwera, anafunsa za momwe aliyense “anapindulitsira pa kuchita malonda.” Ena anachita khama pa kuchita monga mwa lamulo la Mbuye uja, ngakhale panali udani wa “mbadwa” kwa Mbuyeyo. Komabe, kapolo m’modzi anabisa ndalama imodzi ndipo analandira mkwiyo, osati matamando ochokera kwa Mbuye. Tiri ndi fanizo lofanana ndi lomweli la matalente mu Mateyu 25. Mafanizo awiri onsewa amapereka chenjezo la mphamvu kutsutsana ndi kubisa kwa chuma chachikulu cha chowonadi cha Mulungu. Tiyeni potero tiwonetse kulapa kochokera pansi pa mtima penipeni pa zinthu izi, pofunafuna chisomo cha Mulungu mowona mtima kuti chikhulupiriro chathu chiwonjezeredwe. 25. Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo. Mulungu Mzimu Woyera yekha, mwa kuyankha kwa pemphero ndi kulapa kwenikweni, angathe kutiwombola ku machitidwe awa. Kudzera mu pembedzero ndi pemphero mu dzina la Yesu Khristu kuti mipingo komanso munthu aliyense payekha afunefune mwa Mzimu Woyera chisomo, nzeru kulimba mtima ndi madanga a kuchitira umboni kwa Uthenga Wabwino malingana ndi Mawu a Mulungu mu mzimu wa chikondi ndi kudzichepetsa. Tiyeneranso kulingalira za funso iri: kodi Uthenga Wabwino uyenera kulalikidwa kuti. Ndipo kwa yani? Mu mpingo kapena m’kachisi mokha? Timawerenga mu Marko kuti ophunzira “anaturuka, nalalikira ponse ponse, ndipo Ambuye anchita nawo pamodzi, natsimikiza mawu ndi zizindikiro zakutsatapo.” (Marko 16:20). Kotero kodi tingayemebekeze “zizindikiro kutsatira” ngati tisankha malo omwe Uthenga Wabwino uyenera kulalikidwa? Chimodzimodzinso, Mawu a Mulungu amafotokoza momveka bwino kuti Uthenga Wabwino uyenera kulakidwa kwa “olengedwa onse”, ngakhale kuti tachenjezedwa kuti ambiri sadzamva, chifukwa mitima yawo ndiyowumitsidwa. Komabe, sitiyenera kuponyera ngale kwa nkhumba kuti ziponderezedwe pansi pa phazi. (Mateyu 7:6); kuyenera kuti maweruzidwe abwino ndi chitsogozo cha Mzimu kunena mowona ndi zomwe tisowa. Pomaliza, zakhazikitsidwa mu Mateyu 28:19-20 ndi Mawu ena Olembedwa za masakramenti a ubatizo wa okhulupirira ndi chakudya cha Ambuye chomwe chimatchedwanso Mgonero. Tiyenera kukumbukira kuti izi zinakhazikitsidwa ndi Ambuye mwini kuti zitsatidwe ndi okhulupirira onse, omwe amabweretsedwa ndi Mzimu Woyera ku kulapa ndi chikhulupiriro mwa Khristu. Tiyeni tilingalire kuti tanthawuzo lochokera mu buku la Mtanthawuza Mawu lotanthawuza mawu a sakramenti ndi akuti “dongosolo kapena chokhazikitsidwa ndi ulamuliro.” Pokha pokha pamene tiyenda mwa chikhulupiriro mu kumvera Khristu, ndi pomwe Mulungu amalemekezedwa ndi kupatsidwa ulemerero kudzera mwa kuvomereza kwathu kwa dzina Lake. Pomwe pali zambiri zomwe zikananenedwa, tiyenera kumaliza ndi chosowa chofunika kwambiri cha kutsatira Khristu mwa chikhulupiriro, mu chikondi kwa Iyeyo monga Mutu Wamkulu wa mpingo. Ngati mu kudzera mu kusamvera tikuyenda mutsutsana ndi Mulungu, kapena ngati sitikuyenda mu malamulo a Mulungu kudzera mu ulesi, kuwopa munthu, miyambo kapena chifukwa china chiri chonse, titsimikizidwe za ichi, sitidzapita patsogolo 26. Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo. kapena kupindula. Tiyeni tiyike pa mtima Mawu a Khristu pakupemphera mowona mtima kuti tilandire chisomo Chake ndi kuti tilape mowona mtima. Lonjezo lake liri ndi ulamuliro wa uMulungu ndi lotsimikizika, “Ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye ndi iye ndi Ine” (Chivumbulutso 3:20) MUTU 5 ULAMULIRO WA IWO ODZOZEDWA A MULUNGU. Ndondomeko mu Mpingo wa Khristu. Khristu monga Mutu wa mpingo anadzoza atumwi ndi kuwatuma “ndipo pamene Iye anadziyitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu ndi ulamuliro pa mizimu yoyipa yakuyiturutsa, ndi yakuchiza nthenda iri yonse ndi zofowoka zonse.” (Mateyu 10:1). Atakwera Khristu kupita ndi kulowa kumwamba, atumwi anagwiritsa ntchito ulamuliro mu mpingo wa Khristu. Ulamuliro uwu unatengedwa kwa Khristu mwini mwa Mzimu Woyera, ndipo mwakulamulidwa ndi chikumbu mtima chawo kuti athe kugwiritsa ntchito ulamulirowo mwa chikondi ndi mwakumvera Khristu. (2 Akorinto 12:15). Mtumwi Petro chimodzimodzinso akulemba zokhudza iwo omwe ali ndi ulamuliro mu mpingo wa Mulungu. “Akulu tsono mwa inu ndiwadandawulira, ine mkulu mzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nawo ulemerero udzavumbulutsikawo; Wetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokangamiza, koma mwa ufulu, kwa Mulungu, osatsata phindu linyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo. Ndipo pakuwonekera Mbusa wa mkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.” (1 Petro 5:1-4). Nkhani yomwe ikufanizidwa apo ndi ya mbusa yemwe ali pansi pa mbusa wamkulu yemwe akusamalira gawo la busa la Khristu lomwe Iye, monga “Mbusa wa mkulu wazipereka kwa iwo. Chisamaliro ichi chiyenera kuchitika mu chikondi; monga Khristu anawakonda iwo, kuwonetsera mwa miyoyo yawo ndi utumiki chikondi cha Mulungu. Monga Khristu alamulira pa Mpingo mu chikondi, momwenso mbusa wamng’ono alamulire pa busa lomwe iye wapatsidwa kulisamalira mokhulupirika ndi kulamulira mu mphamvu ya chikondi. 27. Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu. Kenaka Petro akulembera kwa iwo omwe ali mamembala a pa busa la nkhosa; “Momwemonso anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.” (1 Ptero 5:1-4). Paulo akulembanso, “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni; pakuti ichi sichikupindulitsani inu”. (Ahebri 13:17). Tikufunafuna kuti tikhazikitse mfundo zoyenera kutsatiridwa apo, posamalitsa kuti mipingo yosiyana iri ndi ndondomeko zawo zawo za mawonekedwe a mpingo, ndi omwe ali ndi ma udindo osiyanasiyana ali ndi mayina omwe adatchulidwa m’Baibulo (mwa chitsanzo mbusa, bishopu, dikoni, kapena mkulu wa mpingo). Ngakhale ziri chomwecho, momwe ndondomeko ya dongosolo iri, liyenera kukhala mogwirizana ndi Mawu Olembedwa. Komabe, tikhoza kupeza pomaliza zotsatira zingapo apa. Sitingayembembekezere kuti tiwone kutuluka kapena kupindula mu mpingo ngati iwo omwe ali pa ma udindo a mpingo alamulira mu nkhanza, kukonda chuma kapena mosakhudzika ndi anthu, poganiza kuti ali “ufulu wa uMulungu” wa mtundu wina wake wakuti akhoza kulamulira mu mpingo monga momwe angafunire ndi kuti azingomvera ziri zonse iwo akulamulira. Pakuchita motero, alibe ulamuliro wa Mulungu mwa njira ina iri yonse. Kapenanso tisayembembekeze kupindula pakudzikuza kuti titsutse iwo omwe ali ndi ulamuliro monga mwa Mawu Olembedwa pa ife. Chifukwa chake, kaya tiri pa gome, pa desiki kapena kumvera otilalikira, pali kusowekera kwa kuyenda kwa wina ali yense payekha ndi Khristu kuti pamenepo pakhale chiyanjano chowona ndiponso umodzi mu mpingo. “Koma ngati tiyenda m’kuwunika, monga Iye ali m’kuwunika, tiyanjana wina ndi mzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.” (1 Yohane 1:7). Nanga tinena kuti chiyani za mipingo imene malo a ma udindo amakhala opanda anthu kwa nthawi yopanda malire eni eni? Kodi tiyembekezere dalitso la Ambuye pomwe ndondomeko ya kumwamba yavumbulutsidwa mu 28. Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu. Mawu a Mulungu sinatsatiridwe? Titenge monga chitsanzo mpingo wopanda mbusa. Nthawi ina kamodzi Khristu anawona unyinji wa anthu; Iye “anagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Marko 6:34). Kotero kuti mipingo isowekera kukhala ndi mbusa kuti aphunzitse Mawu a Mulungu ndi kusamalira nkhosa za pa busa. Ngakhale mu zinthu za ku thupi, nkhosa zopanda mbusa zingathe kusokera mosavuta, kukhala ndi njala, kusocheretsedwa kapena kugwidwa ndi nkhandwe ndi mimbulu. Nanga tingayembekeze bwanji mpingo kuti upindule pomwe palibe mbusa, kapena kufunafuna mwa pemphero ndi chikhumbokhumbo chakukhala ndi m’modzi. Zingathe kunenedwa kuti, “tiyenera kukhutira ndi zinthu zomwe tiri nazo”, koma Mawu Olembedwa awa otengedwa m’Baibulo okhudzana ndi kukwaniritsidwa ndi chuma cha dziko la pansi popewa kukonda chuma, osati kukwaniritsidwa ndi Mawu Olembedwa komwe kukuchitika mu mpingo. Wina angathe kunena kuti, “mpingo wakhala wopanda mbusa kwa zaka zambiri ndipo Ambuye watithandiza kufikira lero.” Inde, izi zisonyeza kuleza mtima ndi chifundo cha Mulungu, koma sitiyenera kuwona kuti zikhoza kumakhala choncho. Zinanenedwanso kuti, “ngati titakhala ndi mbusa, sitingathe kumva atumiki osiyanasiyana omwe ife timakondwera nawo”; inde dziko la pansi limati “kasinthasintha ndiko kukometsa kwa moyo,” koma izi siziyenera kutsatiridwa ndi mpingo. Chowonadi chomveka bwino chochokera mu Mawu Olembedwa ndi ichi, “Ndipo ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha.” (Yeremiya 3:15). Kafukufuku wosabisika wa Mawu a Mulungu amawonetsa kuti udindo wa mbusa uli gawo la ndondomeko ya Mawu Olembedwa (1 Timoteyo 3, Tito 1, Machitidwe a Atumwi 20:17-38). Ngati titafunafuna machitidwe a mtundu wina, tiri pa kuwukira kotsutsana ndi Khristu monga Mutu wa Mpingo. Pamene pali mphatso za ma utumiki ndi mayitanidwe osiyana omwe Mulungu mu mphamvu yake amapereka, monga awo a abusa, aphunzitsi ndi alaliki (Aefeso 4:11), udindo wa abusa unakhazikitsidwa ndi Mulungu kuti upindulire ndi kumangirira mpingo. Izi zimanyalapsyidwa ndi kunyozedwa kotitengera ife ngozi. Ndondomeko mu Banja ndi Dziko. Mawu a Mulungu amakhazikitsa ndondomeko yomveka bwino m’banja, 29. Ulamuliro wa iwo Odzozedwa ndi Mulungu. yomwe yagonera pa chikondi cha nsembe cha Khristu ku Mpingo, ndi kumvera kwa Mpingo kwa chikondi kwa Khristu. “Akazi inu, mverani amuna a inu eni, monga kumvera Ambuye. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Eklesia, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo. Komatu monga Eklesia amvera Khristu, koteronso akazi amvere amuna awo m’zinthu zonse, Amuna inu, kondani akazi anu monganso Khristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwake.” (Aefeso 5;22-25). Nanga ndi chifukwa chiyani chikhalidwe cha masiku ano chatenga malo kwambiri mu mpingo kwa abambo ndi amayi kupanga zowinda zofanana zomwezo, ndi kusiya chowinda cha kumvera m’malo mwa mayi? Kodi nanga iwo omwe avomereza kutsatira Mawu a Mulungu amakakamira pa zowinda zomwe zigwirizana ndi zikhulupiro za ku dziko pa kuzifananiza? Mu nijira zambiri izi zikuchitika kudzera mu umbuli wa Mawu Olembedwa. Koma nanga mayitanidwe okhulupirika a mtumiki wa Uthenga Wabwino? Mwambo wodalitsa ukwati wosatsatira Mawu Olembedwa sungathe kuchitika popanda mbusa kuwalora okwatitsidwa kuti achite malumbiro osokonezedwa amenewa. Ziri m’manja mwa mbusa kuti pakhale kuyakhapo mulandu wa ukulu pamaso pa Mulungu, osakhala pa mwambo wodalitsa ukwati wokhawo, komanso kuti aphunzitse uphungu onse wa Mulungu asanadalitse ukwatiwu. Mu ndondomeko ya ngwiro ya Mulungu ya banja, kumvera kwa mkazi kumalimbikitsidwa ndi chisamaliro cha chikondi cha mwamuna mwa nsembe kwa mkazi wake. Mwamuna ali ndi ulamuliro wa Mawu a Mulungu wakulamulira pa nyumba yake, koma ziyenera kuchitika mwa chikondi. Mwamuna sayenera kulamulira mwa nkhanza, koma yemwe alamulira modzichepetsa. Munthu wa Mulungu m’modzi (yemwe anapita ku ulemerero) anafotokoza moyenera ndi mwachidule kuti fungulo la kukhutitsidwa ndi chisangalalo mu banja ndi mawu akuti “chimwemwe”. Anatenga mawu atatu a chingerezi omwe atanthawuzidwa chimwemwe mu Chichewa, ndipo anati ngati Yesu ali woyambirira, munthu wina (mwamuna kapena mkazi) ali wachiwiri, ndi iweyo ndi wachitatu; apo ndiye kuti padzakhala chimwemwe m’banja, “musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mzake. Mukhale nawo 30. Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu. mtima mkati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 2:3-5). Momwenso, Mawu a Mulungu alamulira ana kuti “amvere akuwabala mwa Ambuye; pakuti ichi ndi chabwino. Lemekeza atate wako ndi amayi ako.” Makolo alamuliridwa kuti asakwiyitse ana awo koma kuti awalere iwo mu m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” Antchito ayenera kumvera ambuye awo; “monga kumvera Khristu,” ndi ambuye ayenera kusamala kusawawopsyeza, “podziwa kuti Ambuye wawo ndi wanu ali M’mwamba.” (Aefeso 6:1-9). Komabe, lero tikuwona kuswedwa kwa kulemekeza kwa ulamuliro wokhazikitsidwa ndi Mulungu. Izi zikuwoneka m’banja, makamaka mwa kufunafuna kwa zinthu kosafuna kukanizidwa kwa onse awiri mwamuna ndi mkazi kuti atsatire ntchito zawo, kuwasiya ana kuti aleredwe ndi kukulitsidwa mu malangizo ndi maweruzo a wayilesi ya kanema, foni ya m’manja, intaneti, kapena za makhalidwe onyansa ndi osapembedza Mulungu. Zikuwonekanso mu mwano womwe antchito amawuwonetsa ku ulamuliro wa ma bwana awo. Mu dziko, Mawu a Mulungu amalamulira kuti mbadwa ziyenera kupereka ulemu woyenera kwa iwo omwe ali mu ulamuliro. Mtumwi Paulo analemba; “Anthu onse amvere ma ulamuliro a akulu, pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu. Kotero kuti iye amene atsutsana nawo ulamuliro, akaniza choyikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza; adzitengera kulanga. Pakuti mafumu sakhala owopsya ntchito zabwino koma zoyipa. Ndipo ufuna kodi kusawopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m’menemo; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choyipa, opatu, Pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa. Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbu mtima. Pakuti chifukwa cha ichi mupatsanso msonkho pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi. Perekani kwa anthu onse mangawa awo, msonkho kwa eni ake msonkho; kulipira kwa eni ake kulipidwa, kuwopa kwa eni ake kuwopa, ulemu kwa eni ake ulemu.” (Aroma 13:1-7). 31. Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu. Kuwonjezera apo, tikuwuzidwa kuti tiyenera kupempherera iwo omwe ali ndi ulamuliro pa ife. “Ndidandawulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapambedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse, chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro, kuti m’moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu, ndi m’kulemekeza monse. Pakuti ichi ndi chokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu.” (1 Timoteyo 2:1-3). Komabe, anthu ambiri mu dziko lino amakhala. Osati pansi pa atsogoleri osapembedza kokha, koma pansi pa iwo omwe amazunza okhulupirira owona. Kotero ndi momwe adachita ndi Paulo mu nthawi yake. Nanga tingatenge kuti Mawu Olembedwa kuti tithe kunena kuti “ayi” kwa iwo omwe ali ndi ulamuliro pa ife mu zinthu zokhudza za dziko la pansi? Mawu a Mulungu akutipatsa ife zitsanzo zomveka bwino mu buku la Danieli. Ana a chiHebri ndi Danieli yemwe nthawi zonse adawonetsa ulemu woyenera ndi kumvera mafumu a ku Babulo ndi Peres. Komatu, pomwe anayitanidwa kuti achite chomwe chinali choletsedwa ndi Mulungu (kulambira mafano) ndi kuti asiye kupemphera kwa Mulungu, motsimikiza mtima ndi mwa ulemu iwo anamvera malamulo a Mulungu, osati malamulo a mfumu ya dziko la pansi. Osasamalira zomwe munthu akadakhoza kuchita motsutsana nawo, Ambuye anayima pambali pawo ndi kuwawombola. Pali phunziro iri la ife lero kuchokera mu Mawu Olembedwa. Mwa tsoka ku Ulaya, tikuwona kuti kuwukira kukunka kukulira kulirabe kwa ana kutsutsa ulamuliro wa makolo awo, mbadwa za dziko kutsutsa atsogoleri omwe aperekedwa kwa iwo, antchito kutsutsa owalemba ntchito, akazi kutsutsa amuna awo, kawiri kawiri pansi pa mbendera ya “ufulu wa chibadwidwe”. Koma mpingo wa Mulungu wovomereza Khristu wayamba kutsatira zinthu izi, tingayembekezere bwanji kuti dziko lisinthe kukhala labwino? Mulungu ali wokwiya mwa chilungamo; ndipo adzafunsa anthu kuti ayankhepo chifukwa cha zinthu izi, komatu makamaka kuchokera kwa ife amene tiri ndi Mawu Ake Olembedwa pamaso pathu, koma kuti sitidayende mu Mawuwo. Koposa kotani nanga kuti adzafuna kwa iwo omwe alalikira zolakwitsa mu mipingo, ndipo ndi utumiki wosakhulupirika okana poyera kuti njira za Mulungu ziri zangwiro! Chisokonezo mu mipingo, m’banja ndi mu dziko zingathe kukonzedwa 32. Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu. mowona ndi mphamvu ya Mzimu Woyera. Pali kusowekera kwakukuru kwa pemphero kuti Uthenga Wabwino udze ndi mphamvu ndi moyo. MUTU 6 CHITSIMIKIZO CHA ULAMULIRO WOTSIRIZA WA MULUNGU. Munthu Ayenera Kuyankhapo Mulandu. Ngakhale kuti timasunga mwa mphamvu za umunthu chiphunzitso cha umwini mphamvu wa Mulungu, momwe munthu wakugwa wasandulitsidwa bwinja “pakufa ku zolakwa ndi uchimo; ndi kufunika kwa ntchito ya Utatu wa uMulungu mu chipulumutso. (Aefeso 1 ndi 2), momwemonso mwa mphamvu timasunga kufotokoza kwa zomwe tachita kwa anthu onse kwa Mulungu. “Pakuti mkwiyo wa Mulungu wochokera Kumwamba, unawonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi chowonadi mchosalungama chawo; chifukwa chodziwika cha Mulungu anachiwonetsera kwa iwo. Pakuti chilengedwere dziko la pansi zawoneka bwino zosawoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi uMulungu wake;, popeza sazindikira ndi zinthu zolenegdwa, kuti iwo adzakhale opanda mawu akuwiringula, chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda pake m’maganizo awo, ndipo unada mtima wawo wopulukira”. (Aroma 1:1821). Mtumwi Petro analemba kuti, “masiku otsiriza onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Liri kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe. Pakuti ichi ayiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidawungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa Mawu a Mulungu.” (2 Petro 3:3-5). Mu Mawu Olembedwa omwe ali pamwambawa tikuwona kuti Mulungu mwa chilungamo amafuna kuti anthu onse apereke kwa Iye ulemerero ndi kuyamikira zoyenera Iye monga Mlengi wawo; koma munthu wakugwa ali nacho chifuniro cha kusamvera ndi kuwukira. Chifukwa cha ichi iwo omwe asiyidwa mu njira zawo zoyipa alibe pokanira. Ndi kudzera mu chisomo choyenera ndi cha ulere cha Mulungu mwa Khristu Yesu kuti ena 33. Chitsimikizo cha Ulamuliro Wotsiriza wa Mulungu. apulumutsidwa, ndi kwa iwo Muwomboli wodalitsika analipira dipo, anasenza chilango ndi kuwawombola iwo ku chiwerezo. (Aroma 9). Anthu onse ayenera kufotokoza za moyo wawo kwa Mulungu, ndipo ayenera kufotokoza za maganizo awo oyipa kwa Iye. Ngakhale tifunafuna kuti tipewe chowonadi ichi cha ulamuliro wa Mulungu pa miyoyo yathu, sitingapewe choyikika cha uMulungu wake “Pakuti kwayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo atafa chiweruzo,” (Ahebri 9:27) “Pakuti ife tonse tidzayima ku mpando wakuweruza wa Mulungu. Pakuti kwalembedwa. Pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malirime onse adzavomereza Mulungu. Chotero munthu ali yense wa ife adzadziwerengera mulandu wake kwa Mulungu.” (Aroma 14:10-12). Kwa anthu a Ambuye, mulandu uwu pamaso pa Mulungu unakonzedwa kudzera mu moyo wolungama ndi nsembe yangwiro ya chimo pa Kalvari ndi Ambuye Yesu Khristu. (Aroma 5 ndi Afilipi 3). Koma timangozitengera kuti ndi momwe zikhalira kuchimwa pang’ono chifukwa Khristu anatiwombola ife? Ngati timamukonda mowonadi Iye, ndi zotsimikizika kuti mowona mtima tikhumba kuti tikhale mfulu ku chimo ndi kulira kamba ka chikhalidwe chathu cha uchimo ndi machimo omwe anamukhomera Iye ku mtanda. Kapena, zidzakhala zochititsa mantha kupezeka kuti “tamupondereza Mwana wa Mulungu” ndipo kenaka “ndi kugwa m’manja mwa Mulungu wamoyo.” (Ahebri 10:10-31) “Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho Chisomo, chimene titumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha. Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.” (Ahebri 12:28-29). Kubwera kwa Chiwiri kwa Khristu. Kubweranso ku dziko la pansi kwa Ambuye Yesu Khristu kudzalengeza za kutha kwa dziko la pansi (Marko 13:24-31). Dziko iri lidzatha pa nthawi imeneyi ndipo ndi njira yomwe Mulungu anayikhazikitsa. Sichiri chakuti munthu angathe kulota kapena mwa kudziwa za kutsogolo mwa nzeru za munthu; koma ziyenera kulandiridwa mwa chikhulupiriro mogwirizana ndi Mawu a Mulungu. Dziko siridzatha mwa chifukwa cha zochitika kwa zinthu pakupita kwa nyengo kwa dziko lonse, kapena siridzatha chifukwa munthu wapumira mpweya wambiri woturuka mwa iye kupita mlengalenga; koma 34. Chitsimikizo cha Ulamuliro Wotsisiriza wa Mulungu. pomwe Khristu adzabwerera mu ulemerero Wake. Potero ife talamulidwa kuti tikhale tcheru ndi kupempherera kubweranso kwa Ambuye. “Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yake sadziwa munthu, angakhale angelo m’Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye. Yang’anirani, dikirani, pempherani, pakuti simudziwa nthawi yake. Monga ngati munthu wa pa ulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu ali yense ntchito yake nalamulira wapakhomo adikire. Chifukwa chake dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yake yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pa usiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa.” (Marko 13:32-35). Kubweranso kwa Khristu kudzakumana ndi kukondwerera kwa anthu Ake owomboledwa , ndi chikondwereronso kumwamba. Kuwonekanso kwake kudzakhala kwa kugonjetsa adani a Mulungu ndi uMulungu. Ngakhale atakhala pa mgwirizano mu mphamvu zawo zonse, sadzapambana. Masomphenya omwe mtumwi Yohane analandira adzakwaniritsidwa mokhudzana ndi Khristu pa kubwera kwake. Mu masomphenyawo Yohane anawona kuti Iye “womkera wotchedwa Wokhulupirika ndi Wowona; ndipo aweruza nachita nkhondo molungama. Ndipo maso ake ali lawi la moto, ndipo pamutu pake pali nduwira za chifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma Iye yekha. Ndipo avala chovala chowazidwa mwazi; ndipo atchedwa dzina lake Mawu a Mulungu.” (Chivumbulutso 19:11-13). Pa kubwera kwa Khristu, monga timawerenga za Iye kuti “adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse ndi mphamvu yomwe. Pakuti Iye ayenera kuchita ufumu kufikira atayika adani onse pansi pa amapazi ake. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.” (1 Akorinto 15:24-26). Khristu ali ndi “zofungulira za imfa ndi hade” ndi “fungulo la Davide,” Iye ali “wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka ndipo palibe wina atsegula. (Chivumbulutso 1:18 ndi 3:7). Ambuye ali ndi ulamuliro wakuwapititsa anthu ochimwa ku chilango chosatha amene afa mu machimo awo, ndiponso ali ndi ulamuliro womwewo kuti atsegule zipata za Yerusalemu wakumwamba kwa iwo omwe ali owomboledwa ndi mwazi Wake wa mtengo wapatali womwe unakhetsedwa pa Kalvari. (Mateyu 25:31-46). 35. Chitsimikizo cha Ulamuliro Wotsiriza wa Mulungu. Ulamuliro wa Khristu monga Mfumu ya mafumu ndi Ambuye wa ambuye udzakhala wa muyaya. Ulamuliro wa Mulungu udzakondwereredwa ndi kutamandidwa ndi onse owomboledwa a Ambuye, adzayika pamaso pa Iye a korona awo. (Chivumbulutso 4:21 ndi 22). Kwa iwo oyipa ndi osatembenuka mtima, malo awo adzakhala Nyanja ya moto Chivumbulutso 20 :11-15), “ndi utsi wa kuzunza kwawo ukwera ku nthawi za nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku” .(Chivumbulutso 14:11). Ulamuliro wa Mulungu uyenera kudzafika pa nthawi yakuti utsimikizidwe kwa muyaya ngakhale mu chiweruzo ndi chowonongeko cha muyaya cha ochimwa. Koma mpingo wowomboledwa, Mkwatibwi wa Khristu, kwa muyaya udzakondwera kukhala womasuka ku mphamvu ya chimo, Satana ndi imfa, ndi kukondwera kuti ayimbe, “Ayenera Mwana wa Nkhosa, wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi ulemerero, ndi chiyamiko.” (Chivumbulutso 5:12). Adzakwera kukhala kwa muyaya pansi pa ulamuliro wa chikondi ndi wa chisomo wa Mfumu ya mafumu. Kumaliza. Tiyenera tsopano kulifikitsa buku laling’onoli ku mapeto. Tafunafuna kuti tifotokoze za mfundo zazikulu za phunziro lathu, mwa zina zambiri zomwe zikadakhoza kukambidwa. Baibulo lonse limalankhula za ulamuliro wa Mulungu kuchokera ku Genesis mpaka ku Chivumbulutso. Ndiye, wowerenga, tikupemphani kuti mwa pemphero mufufuze Mawu Olembedwa, kufunafuna chisomo cha Mulungu ndi kuti chithandizo cha mphamvu yonse cha Mzimu Woyera kukupatsani kuzindikira ndi kuti muyende mu chowonadi. Monga Ambuye Yesu Khristu anena “Indetu ndidza msanga. Amen.” Momwenso ife tibwereze pa kunena; “Idzani, Ambuye Yesu” (Chivumbulutso 22:20). 36. ULAMULIRO WA MULUNGU. Buku ili likuwonetsa phunziro pogwiritsa ntchito Baibulo, Mawu a Mulungu, monga maziko okhawo. Pamene tingawone ochimwa akukaniza ulamuliro wa Mulungu, buku ili linalembedwa mwapadera kwa mamembala ndi atumiki a mipingo. Mu masiku a utumiki wa dziko la pansi wa Ambuye Yesu Khristu, ambiri a anthu a chipembedzo a masiku amenewo adakaniza ulamuliro Wake ndipo “sakadafuna munthu uyu kuti awalamulire” iwo. Mwa tsoka, lero, tikuwona zambiri zofanana ndi zomwezo. Pali mipingo ndi atumiki omwe sadzagwadira ulamuliro wa Mulungu monga wavumbulutsidwa mu Mawu a Mulungu, komatu iwo asankha kufunafuna kuti alowetse m’malo mwake miyambo yawo kapena monga mwa machitidwe a zinthu a dziko la pansi m’malo mwa chiphunzitso cha uMulungu. Ena anyengedwa mwa kuchenjera kwa Satana ndipo ali ambiri omwe ali kufunafuna chowonadi mowona mtima, koma ali ndi mpata wochepa wakuwerenga Baibulo lathunthu kapena zolembedwa za Mawu a Mulungu zomwe ziri za thunthu. Pa chifukwa cha ichi ndi chomwe Free Grace Evangelistic Association iri ndi kukhudzidwa kwa padera. Buku iri lalembedwa kuti lithandize ndi kulangiza iwo omwe akufunafuna kuphunzira za Khristu, ndi omwe akukhumba kuchokera pansi pa mtima kuti alemekeze ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu mu mitima yawo, m’mipingo ndi utumiki. Lirinso chenjezo, kuti tipemphere kuti tigwiritsidwe ntchito mwa mphamvu ndi Mulungu kuti tidzutse ena ali wonse womwe ali mu mdima kapena mu kuwukira. Dr Ian Sadler (BSc, PhD, DLit) ndi Mtsogoleri wa Mkulu wa Free Grace Evangelistic Association wa dziko lonse la pansi ndiponso ndi wa pa Mpando wa Free Grace Evangelistic Association ku Mangalande(Ulaya) komwe ndi ku Likulu . Amakhala ku Ulaya ndipo ndi mtumiki wa mpingo wa Strict Baptist. Ali pa banja ndipo ali ndi ana anayi. Analembanso mabuku ena awa: “Chinsinsicho, Babulo wa Mkulu”, Yesu, ndiye Njira”, ndi “Chikondi cha Mulungu”.
Documentos relacionados
CHA61-1015M Mafunso ndi Mayankho VGR
anapatukana, ena ankafuna kuti akhalebe ndi Mawu, Mawu olembedwa, ena ankafuna mpingo wapamwamba. Izo zinali mu nthawi ya ulamuliro wa Konstantini. Ndipo Konstantini sanali munthu wachipembedzo; iy...
Leia maisubatizo wa mzimu woyera
29 Tsopano, inu mukhoza kutenga chidutswa chaching’ono cha Lemba pano, nkuti, “Yesu anachita zakuti-n-zakuti ndipo ife tiyenera kumachita zomwezo,” inu mukhoza kuwapanga Iwo kunena chirichonse chim...
Leia maisCTK64-0629 Chiuta Mwenenkhongonozose Kuvumbukwa Kwa Ise
muzga, ndipo wakapangika mu chikozgo cha ŵanthu: Ndipo pakuti wakawoneka mu kulingana na munthu, wakajiyuyura yekha, ndipo wakazgoka wakupulikira ku nyifwa, nanga ndi nyifwa ya mphinjika.
Leia mais